RUTE 2
2
Rute akunkha m'munda wa Bowazi
1 #
Mat. 1.5
Ndipo Naomi anali naye mbale wa mwamuna wake, ndiye munthu mwini chuma chambiri wa banja la Elimeleki; dzina lake ndiye Bowazi. 2#Deut. 24.19Nati Rute Mmowabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha la ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomera mtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga. 3Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ochekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Bowazi, ndiye wa banja la Elimeleki. 4#Gen. 43.29Ndipo taona, Bowazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa ocheka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni. 5Nati Bowazi kwa mnyamata woyang'anira ochekawo, Mkazi uyu ngwa yani? 6Ndipo mnyamata woyang'anira ochekawo anayankha nati, Ndiye mkazi Mmowabuyo anabwera ndi Naomi ku dziko la Mowabu; 7ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ochekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo. 8Pamenepo Bowazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakhunkha m'munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno. 9Maso ako akhale pa munda achekawo, ndi kuwatsata; kodi sindinawauza anyamata asakukhudze? Ndipo ukamva ludzu, muka kumitsuko, ukamweko otunga anyamatawo, 10#1Sam. 25.23Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo? 11#Rut. 1.14-17Ndipo Bowazi anayankha nanena naye, Anandifotokozera bwino zonse unachitira mpongozi wako atafa mwamuna wako; ndi kuti wasiya atate wako ndi amai ako, ndi dziko lobadwirako iwe, ndi kudza kwa anthu osawadziwa iwe kale. 12#2Sam. 22.25; Mas. 17.8Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israele, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ake. 13#Gen. 33.15; 50.21Nati iye, Mundikomere mtima mbuye wanga, popeza mwandisangalatsa, popezanso mwanena chokondweretsa mtima wa mdzakazi wanu, ndingakhale ine sindine ngati mmodzi wa adzakazi anu. 14#Rut. 2.18Ndipo pa nthawi ya kudya Bowazi ananena naye, Sendera kuno, nudyeko mkate; nusunse nthongo yako m'vinyo wosasayo. Nakhala iye m'mbali mwa ochekawo; ndipo anamtambasulira dzanja kumninkha tirigu wokazinga, nadya iye, nakhuta, nasiyapo. 15Ndipo ataumirira kukatola khunkha, Bowazi analamulira anyamata ake ndi kuti, Atole khunkha ngakhale pakati pa mitolo, musamchititse manyazi. 16Ndiponso mumtayire za m'manja, ndi kuzisiya, natole khunkha, osamdzudzula. 17Natola khunkha iye m'munda mpaka madzulo; naomba khunkhalo; napeza ngati efa wa barele, 18#Rut. 2.14nalisenza nalowa kumudzi; ndipo mpongozi wake anaona khunkhalo; Rute natulutsanso nampatsa mkute uja anausiya atakhuta. 19#Mas. 41.1Ndipo mpongozi wake ananena naye, Unakatola kuti khunkha lero? Ndi ntchito udaigwira kuti? Adalitsike iye amene anakusamalira. Ndipo anamfotokozera mpongozi wake munthu amene anakagwirako ntchito, nati, Dzina lake la munthuyo ndinakagwirako ntchito lero ndiye Bowazi. 20Nati Naomi kwa mpongozi wake, Yehova amdalitse amene sanaleke kuwachitira zokoma amoyo ndi akufa. Ndipo Naomi ananena naye, Munthuyo ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera cholowa. 21Ndipo Rute Mmowabu anati, Ananenanso nane ndithu, Uwaumirire anyamata anga, mpaka atatha kucheka zanga zonse za m'minda. 22Nati Naomi kwa Rute mpongozi wake, Nchabwino, mwana wanga, kuti uzituluka nao adzakazi ake, ndi kuti asakukomane m'munda wina uliwonse. 23Momwemo anaumirira adzakazi a Bowazi kuti atole khunkha kufikira atatha kucheka barele ndi tirigu; ndipo anakhala iye kwao kwa mpongozi wake.
Currently Selected:
RUTE 2: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi