YouVersion Logo
Search Icon

OBADIYA 1

1
Zoipa zao ndi kulangidwa kwa Aedomu. Dalo la Israele
1 # Ezk. 25.12-14 Masomphenya a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yochokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo. 2Taona, ndakuika wamng'ono mwa amitundu; unyozedwa kwambiri. 3Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani? 4#Yer. 49.16Chinkana ukwera pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, chinkana chisanja chako chisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova. 5Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! Waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akutchera mphesa sadzasiya khunkha kodi? 6Ha! Za Esau zasanthulidwa; ha! Zobisika zake zafunidwa. 7Anthu onse a akupangana nawe anakuperekeza mpaka pamalire; anthu okhala ndi mtendere nawe anakunyenga, nakuposa mphamvu; iwo akudya chakudya chako akutchera msampha pansi pako; mulibe nzeru mwa iye. 8#Yer. 49.7Ati Yehova, Kodi sindidzaononga tsiku lija anzeru mwa Edomu, ndi luntha m'phiri la Esau? 9Ndipo amuna anu amphamvu adzatenga nkhawa, Temani iwe, kuti onse aonongeke m'phiri la Edomu, ndi kuphedwa. 10#Gen. 27.41; Amo. 1.11; Ezk. 35.9Chifukwa cha chiwawa unamchitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzaonongeka kunthawi yonse. 11Tsiku lija unaima padera, tsiku lija alendo anagwira ndende makamu ake, nalowa m'zipata zake achilendo, nachitira Yerusalemu maere, iwenso unakhala ngati mmodzi wa iwowa. 12#Mas. 137.7; Mik. 7.8Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka chikhakha tsiku lakupsinjika. 13Usalowe m'mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe choipa chao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao. 14Ndipo usaime pamphambano kuononga opulumuka ake; kapena kupereka otsala ake tsiku lakupsinjika. 15#Ezk. 30.3; Hab. 2.8Pakuti tsiku la Yehova layandikira amitundu onse; monga unachita iwe, momwemo adzakuchitira; chochita iwe chidzakubwerera pamtu pako. 16#Yer. 25.28-29Pakuti monga munamwa pa phiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo. 17#Yow. 2.32Koma m'phiri la Ziyoni mudzakhala opulumuka, ndipo lidzakhala lopatulika; ndi a nyumba ya Yakobo adzakhala nazo zolowa zao. 18#Zek. 12.6; Zek. 12.6Ndipo nyumba ya Yakobo idzakhala moto, ndi nyumba ya Yosefe lawi, ndi nyumba ya Esau ngati chiputu, ndipo adzawatentha pakati pao, ndi kuwapsereza; ndipo sadzakhalapo otsalira nyumba ya Esau; pakuti Yehova wanena. 19#Amo. 9.12Ndipo akumwera adzakhala nalo phiri la Esau cholowa chao; ndi iwo a kuchidikha adzakhala nalo dziko la Afilisti; ndipo adzakhala nayo minda ya Efuremu, ndi minda ya Samariya cholowa chao; ndi Benjamini adzakhala nalo la Giliyadi. 20Ndipo andende a khamu ili la ana a Israele, okhala mwa Akanani, adzakhala nacho cholowa chao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala m'Sefaradi adzakhala nayo midzi ya kumwera, cholowa chao. 21#Mas. 137.7Ndipo apulumutsi adzakwera pa phiri la Ziyoni kuweruza phiri la Esau; ndipo ufumu udzakhala wake wa Yehova.

Currently Selected:

OBADIYA 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in