YouVersion Logo
Search Icon

YONA Mau Oyamba

Mau Oyamba
Buku la Yona likusiyana ndi mabuku ena a aneneri a mu Baibulo chifukwa likufotokoza mwatsatanetsatane zimene adachita mneneriyo amene sadafune kumvera lamulo la Mulungu. Mulungu anamuuza kuti apite kumzinda wa Ninive, umene unali likulu ka ufumu wamphamvu wa Asiriya, amene anali mdani woipitsitsa wa Aisraele. Koma Yona sanafune kukalalikira uthenga wa Mulungu kumeneko, chifukwa amakhulupirira kuti Mulunguyo sakaononga mzindawo. Patachitika zinthu zingapo zodabwitsa, iyeyo anavomera ndipo pa mapeto ake anakwiya ataona kuti uthenga wake wa chilango sunapherezere.
Bukuli likuonetsa kuti Mulungu ali ndi ulamuliro wonse pa chilengedwe. Komanso likuonetsa kuti Mulungu ndi wachikondi ndi wachifundo, amene amafunitsitsa kukhululukira ndi kupulumutsa adani a anthu ake ngati alapa, osati ndi kuwalanga kapena kuwaononga.
Za mkatimu
Kuitanidwa kwa Yona ndi kusamvera kwake 1.1-17
Yona alapa napulumutsidwa 2.1-10
Uthenga wa Yona wotsutsana ndi Ninive 3.1-10
Chifundo cha Mulungu pa Ninive 4.1-11

Currently Selected:

YONA Mau Oyamba: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in