YouVersion Logo
Search Icon

NEHEMIYA 13

13
Tobiya achotsedwa ku Kachisi
1 # Deut. 23.3-4; 31.11-12 Tsiku lomwelo anawerenga m'buku la Mose m'makutu a anthu, napeza m'menemo kuti Aamoni ndi Amowabu asalowe mu msonkhano wa Mulungu kunthawi yonse; 2#Num. 22.5; 24.10popeza sanawachingamire ana a Israele ndi chakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso. 3Ndipo kunali, atamva chilamulocho, anasiyanitsa pa Israele anthu osokonezeka onse.
4Chinkana ichi, Eliyasibu wansembe, woikidwa asunge zipinda za nyumba ya Mulungu wathu, anachita chibale ndi Tobiya, 5namkonzera chipinda chachikulu, kumene adasungira kale zopereka za ufa, lubani, ndi zipangizo, ndi limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamulidwira Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe. 6#Neh. 5.14Koma pochitika ichi chonse sindinakhala ku Yerusalemu; pakuti chaka cha makumi atatu ndi chachiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu ya Babiloni ndinafika kwa mfumu, ndipo atapita masiku ena ndinapempha mfumu indilole; 7ndipo ndinafika ku Yerusalemu, ndi kuzindikira choipa anachichita Eliyasibu, chifukwa cha Tobiya, ndi kumkonzera chipinda m'mabwalo a nyumba ya Mulungu. 8Ndipo ndinaipidwa nacho kwambiri, motero ndinataya kubwalo akatundu onse a m'nyumba ya Tobiya, kuwachotsa m'chipindamo. 9#2Mbi. 29.5, 15-16, 18Pamenepo ndinalamulira, ndipo anayeretsa zipindazo; ndipo ndinabwezeramonso zipangizo za nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zopereka za ufa ndi lubani. 10#Mala. 3.8-10Ndinazindikiranso kuti sanapereke kwa Alevi magawo ao; m'mwemo Alevi ndi oimbira adathawira yense kumunda wake. 11Potero ndinatsutsana nao olamulira, ndinati, Yasiyidwiranji nyumba ya Mulungu? Ndipo ndinawasonkhanitsa, ndi kuwaika m'malo mwao. 12Ndi Ayuda onse anabwera nalo limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, kunyumba za chuma. 13Ndinaikanso osunga chuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao. 14#Neh. 13.22, 31Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake.
Tsiku la Sabata likhalanso lopatulika
15 # Eks. 20.10; Yer. 17.21-22 Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'choponderamo tsiku la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa abulu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza zilizonse, zimene analowa nazo m'Yerusalemu tsiku la Sabata, ndipo ndinawachitira umboni wakuwatsutsa tsikuli anagulitsa zakudya. 16Anakhalanso m'menemo a ku Tiro, obwera nazo nsomba, ndi malonda ali onse, nagulitsa tsiku la Sabata kwa ana a Yuda ndi m'Yerusalemu. 17#Neh. 13.11Pamenepo ndinatsutsana nao aufulu a Yuda, ndinanena nao, Chinthu chanji choipa ichi muchichita, ndi kuipsa nacho tsiku la Sabata? 18Sanatero kodi makolo anu, ndipo Mulungu wathu anatifikitsira ife ndi mudzi uno choipa ichi chonse? Koma inu muonjezera Israele mkwiyo pakuipsa Sabata. 19Ndipo kunali, kukadayamba chizirezire pa zipata za Yerusalemu, losafika Sabata, ndinawauza atseke pamakomo; ndinawauzanso kuti asatsegulepo, koma litapita Sabata ndipo; ndipo ndinaimika anyamata anga ena pazipata, kuti pasalowe katundu tsiku la Sabata. 20Momwemo eni malonda ndi ogulitsa malonda ali onse, anagona kunja kwa Yerusalemu kamodzi kapena kawiri. 21Koma ndinawachitira umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? Mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikenso pa Sabata. 22#Neh. 12.30; 13.14Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.
Nehemiya awadzudzula pa kukwatira akazi akunja
23 # Ezr. 9.2 Masiku aja ndinaonanso Ayudawo anadzitengera akazi a Asidodi, Aamoni, ndi Amowabu, 24ndi ana ao analankhula mwina Chiasidodi, osadziwitsa kulankhula Chiyuda, koma monga umo amalankhula mtundu wao uliwonse. 25#Neh. 10.29; 13.17Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereka ana anu akazi kwa ana ao amuna, kapena kutengera ana anu amuna, kapena a inu nokha, ana ao akazi. 26#1Maf. 11.1-11Nanga Solomoni mfumu ya Israele sanachimwe nazo zinthu izi? Chinkana mwa amitundu ambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wake anamkonda, ndi Mulungu wake anamlonga mfumu ya Aisraele onse; koma ngakhale iye, akazi achilendo anamchimwitsa. 27#Ezr. 10.2Ndipo kodi tidzamvera inu, kuchita choipa ichi chachikulu chonse, kulakwira Mulungu wathu ndi kudzitengera akazi achilendo? 28Koma wina wa ana a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Muhoroni; chifukwa chake ndinampirikitsa kumchotsa kwa ine. 29#Neh. 6.14Muwakumbukire Mulungu wanga, popeza anadetsa unsembe, ndi pangano la unsembe, ndi la Alevi. 30#Neh. 10.30Momwemo ndinawayeretsa kuwachotsera achilendo onse, ndi kuikira udikiro ansembe ndi Alevi, yense kuntchito yake; 31#Neh. 10.34; 13.22ndi chopereka cha nkhuni pa nthawi zoikika, ndi wa zipatso zoyamba. Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.

Currently Selected:

NEHEMIYA 13: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in