ESTERE Mau Oyamba
Mau Oyamba
Bukuli likukamba za Estere, mtsikana wina wachiyuda, amene ankakonda kwambiri anthu a mtundu wake, naonetsa kulimba mtima kwake pothandiza kuwapulumutsa Ayudawo kwa adani ao. Lifotokozanso za chiyambi chake komanso tanthauzo la chikondwerero cha Chiyuda chotchedwa Purimu.
Za mkatimu
Estere asankhidwa kuti akhale mfumukazi kudziko la Persiya 1.1—2.23
Hamani apanga chiwembu chifuna kuwonongeratu fuko la Ayuda 3.1—5.14
Hamani atsutsidwa naphedwa 6.1—7.10
Ayuda agonjetsa adani ao 8.1—10.3
Currently Selected:
ESTERE Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi