MARKO 7
7
Miyambo ya makolo ao
(Mat. 15.1-20)
1Ndipo anasonkhana kwa Iye Afarisi, ndi alembi ena, akuchokera ku Yerusalemu, 2ndipo anaona kuti ophunzira ake ena anadya mkate ndi m'manja mwakuda, ndiwo osasamba. 3Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu; 4ndipo pakuchoka kumsika, sakudya osasamba m'thupi; ndipo zilipo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa. 5#Mat. 15.2Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda? 6#Yes. 29.13; Mat. 15.8Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa,
Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao,
koma mtima wao ukhala kutali ndi Ine.
7Koma andilambira Iye kwachabe,
ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.
8Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu. 9Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu. 10#Eks. 20.12; Mat. 15.4Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo iye wakunenera zoipa atate wake kapena amai wake, afe ndithu; 11#Mat. 15.5koma inu munena, Munthu akati kwa atate wake, kapena amai wake, Korban, ndiko kuti Mtulo, chimene ukadathandizidwa nacho ndi ine, 12simulolanso kumchitira kanthu atate wake kapena amai wake; 13muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita. 14Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani: 15kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.#7.15 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 16 Amene ali makutu akumva, amve! 17#Mat. 15.15Ndipo m'mene Iye adalowa m'nyumba kusiyana ndi khamulo, ophunzira ake anamfunsa Iye fanizolo. 18Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye; 19chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma m'mimba mwake, ndipo katulukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse. 20Ndipo anati, Chotuluka mwa munthu ndicho chidetsa munthu. 21#Gen. 6.5; 8.21; Mat. 15.8Pakuti m'kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, 22zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: 23zoipa izi zonse zituluka m'kati, nizidetsa munthu.
Mkazi wa Siro-Fenisiya
(Mat. 15.21-28)
24Ndipo Iye anauka nachoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Tiro ndi Sidoni. Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoze kubisika. 25Koma pomwepo mkazi, kabuthu kake kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake. 26Koma mkaziyo anali Mgriki, mtundu wake Msiro-Fenisiya. Ndipo anampempha Iye kuti atulutse chiwanda m'mwana wake. 27Ndipo ananena naye, Baleka, athange akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana, ndi kuutayira tiagalu. 28Koma iye anavomera nanena ndi Iye, Ine Ambuye; tingakhale tiagalu ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana. 29Ndipo anati kwa iye, Chifukwa cha mau amene, muka; chiwanda chatuluka m'mwana wako wamkazi. 30Ndipo anachoka kunka kunyumba kwake, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi chiwanda chitatuluka.
Yesu achiritsa munthu wogontha ndi wosalankhula
31 #
Mat. 15.29
Ndipo anatulukanso m'maiko a ku Tiro, nadzera pakati pa Sidoni, kufikira ku nyanja ya Galileya, ndi kupyola pakati pa maiko a ku Dekapoli. 32Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wachibwibwi; ndipo anampempha Iye kuti aike dzanja pa iye. 33#Mrk. 8.23; Yoh. 9.6Ndipo anampatula pa khamu la anthu pa yekha, nalonga zala zake m'makutu mwake, nalavula malovu, nakhudza lilime lake: 34#Yoh. 11.33, 38nagadamira kumwamba, nausa moyo, nanena naye, Efata, ndiko, Tatseguka. 35#Yes. 35.5-6Ndipo makutu ake anatsegula, ndi chomangira lilime lake chinamasulidwa, ndipo analankhula chilunjikire. 36#Mrk. 5.43Ndipo anawalamulira kuti asauze munthu aliyense; koma monga momwe Iye anawalamulitsa momwenso makamaka analalikira kopambana. 37Ndipo anadabwa kwakukulukulu, nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.
Currently Selected:
MARKO 7: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi