MARKO 6
6
Apeputsa Yesu ku Nazarete
(Mat. 13.53-56; Luk. 4.16-30)
1Ndipo Iye anatuluka kumeneko; nafika kudziko la kwao; ndipo ophunzira ake anamtsata. 2#Yoh. 6.42Ndipo pofika tsiku la Sabata, anayamba kuphunzitsa m'sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake? 3#Mat. 11.6; 12.46Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye. 4Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ake, ndi m'nyumba yake. 5#Gen. 19.22; 32.25; Mat. 13.58Ndipo kumeneko sanakhoze Iye kuchita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ake pa anthu odwala owerengeka, nawachiritsa. 6#Yes. 59.16; Mat. 9.35Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.
Yesu atuma khumi ndi awiriwo
(Mat. 10.1, 5, 9-14; Luk. 9.1-5; 10.4-11)
7 #
Luk. 9.1
Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiriawiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa; 8ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m'lamba lao; 9koma avale nsapato; ndipo anati, Musavale malaya awiri. 10#Luk. 9.4; 10.7-8Ndipo ananena nao, Kumene kulikonse mukalowa m'nyumba, khalani komweko kufikira mukachokako. 11#Luk. 10.10-11; Mac. 13.51Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakuchoka kumeneko, sansani fumbi lili kumapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo. 12Ndipo anatuluka nalalikira kuti anthu atembenuke mitima. 13#Yak. 5.14Ndipo anatulutsa ziwanda zambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala, nawachiritsa.
Kuphedwa kwa Yohane Mbatizi
(Mat. 14.1-12; Luk. 3.19-20; 9.7-9)
14Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye. 15#Mat. 16.14Koma ena ananena, kuti, Ndiye Eliya. Anati enanso, Ndiye mneneri, monga ngati mmodzi wa aneneriwo. 16Koma Herode pamene anamva, ananena, Yohane amene ndamdula mutu, wauka iyeyo. 17Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m'nyumba yandende, chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye. 18#Lev. 18.16Pakuti Yohane adanena kwa Herode, Si kuloledwa kwa inu kukhala naye mkazi wa mbale wanu. 19Ndipo Herodiasi anamuda, nafuna kumupha; koma sanakhoze; 20pakuti Herode anaopa Yohane, podziwa kuti ali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo anamsunga iye. Ndipo pamene anamva iye anathedwa nzeru, nakondwa kumva iye. 21#Gen. 40.20Ndipo pamene panafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, iye anawakonzera phwando akulu ake ndi akazembe ake ndi anthu omveka a ku Galileya; 22ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiasi analowa yekha navina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pachakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine chilichonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe. 23#Est. 5.3, 6Ndipo anamlumbirira iye, kuti, Chilichonse ukandipempha ndidzakupatsa, kungakhale kukugawira ufumu wanga. 24Ndipo anatuluka, nati kwa amake, Ndidzapempha chiyani? Ndipo iye anati, Mutu wake wa Yohane Mbatizi. 25Ndipo pomwepo analowa m'mangum'mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wake wa Yohane Mbatizi mumbale. 26Ndipo mfumu inamva chisoni chachikulu; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo akukhala pachakudya, sanafune kumkaniza. 27Ndipo pomwepo mfumu inatuma mnyamata, namlamulira akatenge mutu wake; ndipo iye anamuka namdula mutu m'nyumba yandende; 28natengera mutu wake mumbale, naupereka kwa buthulo; ndipo buthu linaupereka kwa amake. 29Ndipo m'mene ophunzira ake anamva, anadza nanyamula mtembo wake nauika m'manda.
Yesu achulukitsa mikate
(Mat. 14.13-21; Mrk. 8.1-10; Luk. 9.10-17; Yoh. 6.1-13)
30Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa. 31Ndipo Iye ananena nao, idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi. Pakuti akudza ndi akuchoka anali piringupiringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya. 32Ndipo anachokera m'ngalawa kunka kumalo achipululu padera. 33Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikira, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ochokera m'midzi monse, nawapitirira. 34#Mat. 9.36Ndipo anatuluka Iye, naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri. 35#Luk. 9.12Ndipo pamene dzuwa lidapendeka ndithu, anadza kwa Iye ophunzira ake, nanena, Malo ano nga chipululu, ndi dzuwa lapendeka ndithu; 36muwauze kuti amuke, alowe kumilaga ndi kumidzi yozungulira, akadzigulire okha kanthu kakudya. 37#Num. 11.13, 22-23Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya? 38Ndipo Iye ananena nao, kuti, Muli nayo mikate ingati? Pitani, mukaone. Ndipo m'mene anadziwa ananena, Isanu, ndi nsomba ziwiri. 39Ndipo anawalamulira kuti akhalitse pansi onse magulumagulu pamsipu. 40Ndipo anakhala pansi mabungwemabungwe a makumi khumi, ndi a makumi asanu. 41#1Sam. 9.13; Mat. 26.26Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang'ana kumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo. 42Ndipo anadya iwo onse, nakhuta. 43Ndipo anatola makombo, madengu khumi ndi iwiri, ndiponso za nsomba. 44Ndipo amene anadya mikate iyo anali amuna zikwi zisanu.
Yesu ayenda pa nyanja
(Mat. 14.22-36; Yoh. 6.15-25)
45Ndipo pomwepo Iye anakakamiza ophunzira ake alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m'mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke. 46Ndipo atalawirana nao, anachoka Iye, nalowa m'phiri kukapemphera. 47#Mat. 14.23Ndipo pofika madzulo ngalawa inali pakati pa nyanja, ndi Iye yekha pamtunda. 48#Luk. 24.28Ndipo pakuwaona ali kuvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa ulonda wachinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire; 49koma iwo, pamene anamuona alikuyenda panyanja, anayesa kuti ndi mzukwa, nafuula: 50pakuti iwo onse anamuona Iye, nanthunthumira. Koma pomwepo anawalankhula nanena nao, Limbani mtima; ndinetu, musaope. 51Ndipo Iye anakwera, nalowa kwa iwo m'ngalawa, ndipo mphepo inaleka; ndipo anadabwa kwakukulu mwa iwo okha; 52#Mrk. 8.17-18pakuti sanazindikire za mikateyo, koma mitima yao inauma.
53 #
Mat. 14.34
Ndipo ataoloka iwo, anafika pamtunda ku Genesarete, nakocheza padooko. 54Ndipo pamene anatuluka m'ngalawa anamzindikira pomwepo, 55nathamangira dziko lonselo nayamba kunyamula anthu odwala pa mphasa zao, kufika nao kumene anamva kuti analiko Iye. 56#Mat. 9.20; Mac. 19.12Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena m'milaga, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.
Currently Selected:
MARKO 6: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi