MATEYU 8
8
Yesu achiritsa wakhate
(Mrk. 1.40-45; Luk. 5.12-14)
1Ndipo pakutsika pake paphiripo, inamtsata mipingo yambiri ya anthu. 2Ndipo onani, wakhate anadza namgwadira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza. 3Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka. 4#Mat. 9.30; Mrk. 5.43; Lev. 14.3-4, 10Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo.
Kenturiyo wa ku Kapernao
(Luk. 7.1-10)
5Ndipo m'mene Iye analowa m'Kapernao anadza kwa Iye kenturiyo, nampemba Iye, 6nati, Ambuye, mnyamata wanga ali gone m'nyumba wodwala manjenje, wozunzidwa koopsa. 7Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamchiritsa iye. 8#Mas. 107.20; Luk. 7.2; 15.19, 21Koma kenturiyoyo anavomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa chindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga. 9Pakuti inenso ndili munthu wakumvera ulamuliro, ndili nao asilikali akundimvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndi kwa kapolo wanga, Chita ichi, nachita. 10Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeza chikhulupiriro chotere. 11#Mala. 1.11; Luk. 13.29; Aef. 3.6Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba; 12#Mat. 21.43; Luk. 13.28koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. 13#Mat. 9.29Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anachiritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo.
Mpongozi wa Petro
(Mrk. 1.29-34; Luk. 4.38-41)
14 #
Mrk. 1.29-31
Ndipo pofika Yesu kunyumba ya Petro, anaona mpongozi wake ali gone, alikudwala malungo. 15Ndipo anamkhudza dzanja lake, ndipo malungo anamleka mkaziyo; ndipo anauka, namtumikira Iye.
16 #
Mrk. 1.32-34
Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse; 17#Yes. 53.4kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti,
Iye yekha anatenga zofooka zathu,
nanyamula nthenda zathu.
Matsatidwe ake a Yesu
(Luk. 9.57-60)
18Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamulira ophunzira amuke kutsidya lina. 19#Luk. 9.57-58Ndipo anadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kulikonse mumukako. 20Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.
21 #
1Maf. 19.20
Ndipo wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, mundilole ine nditange ndamuka kuika maliro a atate wanga. 22Koma Yesu ananena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa aike akufa ao.
Yesu aletsa namondwe
(Mrk. 4.35-41; Luk. 8.22-25)
23Ndipo pamene Iye atalowa m'ngalawa, ophunzira ake anamtsata Iye. 24#Mrk. 4.37Ndipo onani, panauka namondwe wamkulu panyanja, kotero kuti ngalawa inafundidwa ndi mafunde: koma Iye anali m'tulo. 25Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tilikutayika. 26#Mas. 65.7Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikulu. 27Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
Ogwidwa ndi ziwanda a ku Gadara
(Mrk. 5.1-17; Luk. 8.26-37)
28 #
Mrk. 5.1-5
Ndipo pofika Iye kutsidya lina, kudziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapo munthu pa njira imeneyo. 29#1Maf. 17.18; Mac. 16.39Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike? 30Ndipo panali patali ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya. 31Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m'gulu la nkhumbazo. 32Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inatuluka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi. 33Koma akuziweta anathawa, namuka kumidzi, nauza zonse, ndi zakuti zao za aziwanda aja. 34#1Maf. 17.18; Mac. 16.39Ndipo onani, mudzi wonse unatulukira kukakumana naye Yesu, ndipo m'mene anamuona Iye, anampempha kuti achoke m'malire ao.
Currently Selected:
MATEYU 8: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi