MATEYU 7
7
Za kuweruza mnzake, kulimbika m'kupemphera, zipata ziwiri, aneneri onyenga, kumva ndi kuchita
1 #
Luk. 6.37-42; Aro. 2.1 Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. 2#Mrk. 4.24Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso. 3Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira? 4Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli. 5Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako.
6 #
Mac. 13.45-46
Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.
7 #
Luk. 11.9-13; Mrk. 11.24; 1Yoh. 3.22 Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu; 8#Luk. 11.9-13; Mrk. 11.24; 1Yoh. 3.22pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa. 9Kapena munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wake mkate, adzampatsa mwala? 10Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? 11Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye? 12#Luk. 6.31; Aro. 13.8-10Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.
13Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. 14#Luk. 13.24Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.
15 #
Deut. 13.1, 3; Mrk. 13.22; Aro. 16.17, 18; 1Yoh. 4.1 Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa. 16#Luk. 6.43, 44Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? 17#Luk. 6.43, 44Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. 18#Luk. 6.43, 44Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. 19#Luk. 3.9Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. 20Inde chomwecho pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.
21 #
Hos. 8.2-4; Luk. 6.46; 13.25-27; Aro. 2.13 Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba. 22#1Ako. 13.2Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri? 23#Mat. 25.12; Luk. 13.25-27; 2Tim. 2.19Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika. 24#Mat. 7.24-27; Luk. 6.47-49Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; 25ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwa; chifukwa inakhazikika pathanthwepo. 26Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; 27ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.
28 #
Mrk. 1.22; Luk. 4.32; Yoh. 7.46 Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: 29pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembi ao.
Currently Selected:
MATEYU 7: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi