1
MATEYU 7:7
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu
Compare
Explore MATEYU 7:7
2
MATEYU 7:8
pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.
Explore MATEYU 7:8
3
MATEYU 7:24
Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe
Explore MATEYU 7:24
4
MATEYU 7:12
Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.
Explore MATEYU 7:12
5
MATEYU 7:14
Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.
Explore MATEYU 7:14
6
MATEYU 7:13
Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho.
Explore MATEYU 7:13
7
MATEYU 7:11
Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?
Explore MATEYU 7:11
8
MATEYU 7:1-2
Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.
Explore MATEYU 7:1-2
9
MATEYU 7:26
Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga
Explore MATEYU 7:26
10
MATEYU 7:3-4
Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira? Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli.
Explore MATEYU 7:3-4
11
MATEYU 7:15-16
Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?
Explore MATEYU 7:15-16
12
MATEYU 7:17
Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa.
Explore MATEYU 7:17
13
MATEYU 7:18
Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma.
Explore MATEYU 7:18
14
MATEYU 7:19
Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto.
Explore MATEYU 7:19
Home
Bible
Plans
Videos