YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 13

13
Fanizo la Wofesa
(Mrk. 4.1-20; Luk. 8.4-15)
1 # Mrk. 4.1 Tsiku lomwelo Yesu anatuluka m'nyumbamo, nakhala pansi m'mbali mwa nyanja. 2#Luk. 8.4Ndipo makamu ambiri a anthu anasonkhanira kwa Iye, kotero kuti Iye analowa m'ngalawa, nakhala pansi, ndipo khamu lonse linaima pamtunda. 3#Luk. 8.5Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu. 4Ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nizilusira izo. 5Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhala nalo dothi lakuya. Ndipo m'mene dzuwa linakwera zinapserera; 6ndipo popeza zinalibe mizu zinafota. 7Koma zina zinagwa paminga, ndipo mingayo inayanga, nizitsamwitsa izo. 8Koma zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu. 9#Mat. 11.15; Mrk. 4.9Amene ali ndi makutu, amve.
10Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Chifukwa chanji muphiphiritsira iwo m'mafanizo? 11#Mat. 16.17; Mrk. 4.11; 1Ako. 2.10Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo. 12#Mat. 25.29Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zochuluka; koma yense amene alibe, chingakhale chomwe ali nacho chidzachotsedwa kwa iye. 13Chifukwa chake ndiphiphiritsira iwo m'mafanizo; chifukwa kuti akuona samaona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa. 14#Yes. 6.9-10; Mrk. 4.12; Luk. 8.10Ndipo adzachitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati,
Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse;
pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse.
15 # Yes. 6.9-10; Mrk. 4.12; Luk. 8.10 Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa,
ndipo m'makutu ao anamva mogontha,
ndipo maso ao anatsinzina;
kuti asaone konse ndi maso,
asamve ndi makutu,
asazindikire ndi mtima wao,
asatembenuke,
ndipo ndisawachiritse iwo.
16 # Luk. 10.23-24 Koma maso anu ali odala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva. 17#Aheb. 11.13; 1Pet. 1.10-11Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama analakalaka kupenya zimene muzona, koma sanazione; ndi kumva zimene muzimva, koma sanazimve.
Kumasulira kwa fanizo la wofesa
(Mrk. 4.14-30)
18 # Mrk. 4.14 Ndipo tsono mverani inu fanizolo la wofesa mbeu uja. 19Munthu aliyense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira. 20Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mau, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera; 21ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo chifukwa cha mau, iye akhumudwa pomwepo. 22Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso. 23Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.
Fanizo la namsongole
24Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake; 25koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo. 26Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole. 27Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo? 28Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wachichita ichi. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse uyo pamodzi? 29Koma iye anati, Iai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye. 30Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.
Fanizo la kambeu kampiru ndi la chotupitsa mkate
(Mrk. 4.30-34; Luk. 13.18-21)
31 # Mrk. 4.30 Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi kambeu kampiru, kamene anakatenga munthu, nakafesa pamunda pake; 32kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakulu kuposa zitsamba zonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nizibindikira mu nthambi zake.
33 # Luk. 13.20-21 Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.
34 # Mrk. 4.33-34 Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu a anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhule kanthu kwa iwo; 35#Mas. 78.2; Aro. 16.25-26kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri, kuti,
Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo;
ndidzawulula zinthu zobisika
chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi.
Yesu awatanthauzira fanizo la namsongole
36Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda. 37Ndipo Iye anayankha nati, Wofesa mbeu yabwino ndiye Mwana wa Munthu; 38#Mat. 24.14; 28.19; Yoh. 8.44; Mac. 13.10; Aro. 10.18Ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo; 39#Chiv. 14.15ndipo mdani amene anamfesa uwu, ndiye mdierekezi: ndi kututa ndicho chimaliziro cha nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo. 40Ndipo monga namsongole asonkhanitsidwa pamodzi, natenthedwa pamoto, motero mudzakhala m'chimaliziro cha nthawi ya pansi pano. 41Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika, 42#Mat. 8.12; Chiv. 19.20ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. 43#Dan. 12.3; Mat. 13.9Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve.
Fanizo la chuma chobisika, la ngale, la khoka
44 # Afi. 3.7-8 Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m'munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m'kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.
45Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino: 46ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.
47 # Mat. 22.10 Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m'nyanja, ndi kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse; 48limene podzala, analivuulira pamtunda; ndipo m'mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m'zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo. 49#Mat. 25.32Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino, 50nadzawataya m'ng'anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
51Mwamvetsa zonsezi kodi? Iwo anati kwa Iye, Inde. 52Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake, mlembi aliyense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m'chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano.
Ampeputsa Yesu ku Nazarete
(Mrk. 6.1-6)
53Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anachokera kumeneko. 54#Mrk. 6.1Ndipo pofika kudziko la kwao, anaphunzitsa iwo m'sunagoge mwao, kotero kuti anazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu izi? 55#Mat. 12.46; Mrk. 6.3; 15.40; Yoh. 6.42Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? Kodi dzina lake la amake si Maria? Ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda? 56Ndipo alongo ake sali ndife onsewa? Ndipo Iyeyo adazitenga zinthu zonsezi kuti? 57#Luk. 8.24; Yoh. 4.44Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu koma kudziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwake. 58Ndipo Iye, chifukwa cha kusakhulupirira kwao, sanachite kumeneko zamphamvu zambiri.

Currently Selected:

MATEYU 13: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in