YouVersion Logo
Search Icon

YOSWA 22

22
A fuko la Rubeni, la Gadi, ndi la Manase logawika pakati amuka kwao
1Pamenepo Yoswa anaitana Arubeni ndi Agadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, 2#Num. 32.20-22nanena nao, Mwasunga inu zonsezo anakulamulirani Mose mtumiki wa Yehova; mwamveranso mau anga m'zonse ndinakulamulirani inu; 3simunasiya abale anu masiku awa ambiri mpaka lero lino, koma mwasunga chisungire lamulo la Yehova Mulungu wanu. 4#Num. 32.33Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mukani ku mahema anu, ku dziko la cholowa chanu chimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordani. 5#Deut. 10.12Koma samalirani bwino kuti muchite chilangizo ndi chilamulo zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake zonse ndi kusunga malamulo ake, ndi kumuumirira Iye, ndi kumtumikira Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. 6Momwemo Yoswa anawadalitsa, nawauza amuke; ndipo anamuka ku mahema ao. 7Ndipo gawo limodzi la fuko la Manase, Mose anawapatsa cholowa m'Basani; koma gawo lina Yoswa anawaninkha cholowa pakati pa abale ao tsidya lija la Yordani kumadzulo. Ndiponso pamene Yoswa anawauza amuke ku mahema ao, anawadalitsa; 8#Yos. 1.7nanena nao ndi kuti, Bwererani nacho chuma chambiri ku mahema anu, ndi zoweta zambirimbiri, ndi siliva, ndi golide, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi malaya ambirimbiri; mugawane nao abale anu zofunkha kwa adani anu.
9Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anabwerera, nachoka kwa ana a Israele ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kunka ku dziko la Giliyadi, ku dziko laolao, limene anakhala eni ake, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.
Guwa la nsembe la umboni
10Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordani, ndilo la m'dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anamanga ku Yordani guwa la nsembe, guwa lalikulu maonekedwe ake. 11Ndipo ana a Israele anamva anthu akuti, Taonani ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anamanga guwa la nsembe pandunji pa dziko la Kanani, ku mbali ya ku Yordani, ku mbali ya ana a Israele. 12Pamene ana a Israele anamva ichi msonkhano wonse wa ana a Israele anasonkhana ku Silo, kuti awakwerere kuwathira nkhondo.
13Ndipo ana a Israele anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, ku dziko la Giliyadi, Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, 14ndi akalonga khumi naye; nyumba imodzi ya atate kalonga mmodzi, kotero ndi mafuko onse a Israele; yense wa iwowa ndiye mkulu wa nyumba ya atate ao mwa mabanja a Israele. 15M'mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, ku dziko la Giliyadi, ananena nao ndi kuti, 16Utero msonkhano wonse wa Yehova, Cholakwa ichi nchiyani mwalakwira nacho Mulungu wa Israele, ndi kumtembenukira Yehova lero lino kusamtsatanso, popeza munadzimangira guwa la nsembe kupikisana ndi Yehova lero lino? 17#Num. 25.3-4Kodi mphulupulu ya ku Peori itichipera, imene sitinadziyeretsera mpaka lero lino, ungakhale mliri unadzera msonkhano wa Yehova, 18kuti mubwerera lero lino kusatsata Yehova? Ndipo kudzakhala kuti popeza lero mupikisana ndi Yehova, mawa adzakwiyira msonkhano wonse wa Israele. 19#Yos. 18.1Koma mukayesa dziko la cholowa chanu nchodetsa, olokani kulowa m'dziko la cholowa cha Yehova m'mene chihema cha Yehova chikhalamo, nimukhale nacho cholowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu. 20#Yos. 7.1, 5Kodi Akani mwana wa Zera sanalakwe m'choperekedwacho, ndipo mkwiyo unagwera msonkhano wonse wa Israele? Osangoonongeka yekha munthuyo mu mphulupulu yake.
21Pamenepo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anayankha, nanena ndi akulu a mabanja a Israele, 22#1Maf. 8.39Yehova Chauta Mulungu, Yehova Chauta Mulungu, Iye adziwa, ndi Israele adzadziwa; ngati mopikisana, ngati molakwira Yehova, 23tadzimangira guwa la nsembe, kubwerera kusamtsata Yehova, musatipulumutsa lero lino; kapena ngati kufukizapo nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa, kapena kuperekapo nsembe zoyamika, achifunse Yehova mwini wake; 24ndipo ngati ife sitinachita ichi chifukwa cha kuopa mlandu, ndi kuti, Masiku akudzawo ana anu akadzanena ndi ana athu, ndi kuti, Muli chiyani inu kwa Yehova Mulungu wa Israele? 25Pakuti Yehova anaika Yordani ukhale malire pakati pa ife ndi inu, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi; mulibe gawo ndi Yehova; motero ana anu adzaleketsa ana athu asaope Yehova. 26Chifukwa chake tinati, Tiyeni tikonzeretu zotimangira guwa la nsembe, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai; 27#Gen. 31.48koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu, ndi pakati pa mibadwo yathu ya m'tsogolo, kuti tikachita ntchito ya Yehova pamaso pake ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m'tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova. 28Chifukwa chake tinati, Kudzali, akadzatero kwa ife, kapena kwa mibadwo yathu m'tsogolomo, kuti tidzati, Tapenyani, chitsanzo cha guwa la nsembe la Yehova, chomanga makolo athu, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai, koma ndilo mboni pakati pa ife ndi inu. 29Sikungatheke kuti tipikisane ndi Yehova ndi kubwerera lero kusatsata Yehova, kumanga guwa la nsembe la kufukizapo nsembe yopsereza, la nsembe yaufa, kapena yophera, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu lokhala pakhomo pa chihema chake.
30Pamene Finehasi wansembe, ndi akalonga a msonkhano ndi akulu a mabanja a Israele okhala naye anamva mau adawanena ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, anawakomera pamaso pao. 31#2Mbi. 15.2Ndipo Finehasi, mwana wa Eleazara wansembe ananena ndi ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, lero lino tidziwa kuti Yehova ali pakati pa ife, pakuti simunalakwira nacho Yehova; tsopano mwalanditsa ana a Israele m'dzanja la Yehova. 32Ndipo Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, ndi akalonga anabwerera kuchokera kwa ana a Rubeni, ndi kwa ana a Gadi, m'dziko la Giliyadi, kudza ku dziko la Kanani kwa ana a Israele, nawabwezera mau. 33#1Mbi. 29.11, 20; Neh. 8.6Ndipo mauwo anakomera ana a Israele pamaso pao; ndi ana a Israele analemekeza Mulungu, osanenanso za kuwakwerera ndi kuwathira nkhondo, kuliononga dziko lokhalamo ana a Rubeni ndi ana a Gadi. 34#Yos. 22.27Ndipo ana a Rubeni ndi ana a Gadi analitcha guwa la nsembelo: Ndilo mboni pakati pa ife kuti Yehova ndiye Mulungu.

Currently Selected:

YOSWA 22: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YOSWA 22