YOSWA 1
1
1 #
Aheb. 3.5
Ndipo atafa Mose mtumiki wa Yehova, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mnyamata wa Mose, 2Mose mtumiki wanga wafa; tauka tsono, nuoloke Yordani uyu, iwe ndi anthu awa onse, kulowa m'dzikomo ndilikuwapatsa, ndiwo ana a Israele. 3#Deut. 11.24Pali ponse phazi lanu lidzapondapo ndinakupatsani, monga ndinanena ndi Mose. 4#Num. 34.3-12Kuyambira chipululu, ndi Lebanoni uyu, kufikira mtsinje waukulu mtsinje wa Yufurate, dziko lonse la Ahiti, ndi kufikira Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa, ndiwo malire anu. 5#Eks. 3.12; Deut. 31.6, 8Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya. 6#Deut. 31.7Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikoli likhale cholowa chao, ndilo limene ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa. 7Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipatukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako. 8#Deut. 17.18-19; Mas. 1.2Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru. 9#Yos. 1.6-7Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.
10Pamenepo Yoswa analamulira akapitao a anthu, ndi kuti, 11Pitani pakati pa chigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordani uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanulanu. 12Ndipo Yoswa anati kwa Arubeni, ndi Agadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, ndi kuti, 13#Num. 32.20-28Kumbukirani mau amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani inu, kuti, Yehova Mulungu wanu akupatsani mpumulo, nadzakupatsani dziko lino. 14Akazi anu, ana anu, ndi zoweta zanu zikhale m'dzikoli anakuninkhani Mose, tsidya lino la Yordani; koma inu muoloke okonzeka kunkhondo pamaso pa abale anu, ngwazi zonse, ndi kuwathandiza; 15#Yos. 22.4mpaka Yehova atapatsa abale anu mpumulo, monga umo anakuninkhirani inu, naonso alandira dzikolo awaninkha Yehova Mulungu wanu; pamenepo mubwerere ku dziko lanulanu, ndi kukhala nalo, limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya lino la Yordani la kum'mawa, 16Ndipo anamyankha Yoswa, nati, Zonse mwatilamulira tidzachita, ndipo kulikonse mutitumako tidzamuka. 17#1Maf. 1.37Monga momwe tinamvera mau onse a Mose momwemo tidzamvera inu; komatu akhale ndi inu Yehova Mulungu wanu monga anakhala ndi Mose. 18Aliyense wakupikisana ndi inu, osamvera mau anu mulimonse mukamlamulira, aphedwe; komatu khalani wamphamvu, nimulimbike mtima.
Currently Selected:
YOSWA 1: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi