YouVersion Logo
Search Icon

YONA 1

1
Kuitanidwa kwa Yona, kuthawa kwake, ndi kulangidwa kwake
1 # 2Maf. 14.25 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona mwana wa Amitai, ndi kuti, 2#Gen. 10.11-12; 18.20-21Nyamuka, pita ku Ninive, mudzi waukuluwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga. 3#Mac. 9.36Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisisi, napereka ndalama zake, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisisi kuzemba Yehova. 4Koma Yehova anautsa chimphepo chachikulu panyanja, ndipo panali namondwe wamkulu panyanja, ndi chombo chikadasweka. 5#Mac. 27.18-19Pamenepo amalinyero anachita mantha, nafuulira yense kwa mulungu wake, naponya m'nyanja akatundu anali m'chombo kuchipepuza. Koma Yona adatsikira m'munsi mwa chombo, nagona tulo tofa nato. 6#Mas. 120.1Ndipo mwini chombo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam'tulo? Uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukira tingatayike. 7#Yos. 7.14, 16; Mac. 1.26Ndipo anati yense kwa mnzake, Tiyeni tichite maere, kuti tidziwe choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani. M'mwemo anachita maere, ndipo maere anagwera Yona. 8#Yos. 7.19Pamenepo anati kwa iye, Utiuzetu choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani? Ntchito yako njotani? Ufumu kuti? Dziko lako nliti? Nanga mtundu wako? 9Ndipo ananena nao, Ndine Muhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda. 10Pamenepo amunawo anaopa kwambiri, nati kwa iye, Ichi nchiyani wachichita? Pakuti amunawo anadziwa kuti anathawa pamaso pa Yehova, popeza adawauza. 11Tsono anati kwa iye, Tichitenji nawe, kuti nyanja itichitire bata? Popeza namondwe anakulakulabe panyanja. 12#Yoh. 11.50Ndipo anati nao, Mundinyamule ndi kundiponya m'nyanja, momwemo nyanja idzachitira inu bata; pakuti ndidziwa kuti namondwe wamkulu amene wakugwerani chifukwa cha ine. 13Koma amunawo anapalasa kubwerera kumtunda, koma sanathe; pakuti namondwe wa panyanja anakulakula mokomana nao. 14Pamenepo anafuulira kwa Yehova, nati, Tikupemphanitu, Yehova, tisatayike chifukwa cha moyo wa munthu uyu, musatisenzetse mwazi wosachimwa; pakuti, Inu Yehova, mwachita monga mudakomera Inu. 15#Luk. 8.24Momwemo ananyamula Yona, namponya m'nyanja; ndipo nyanja inaleka kukokoma kwake. 16#Mrk. 4.41Ndipo amunawo anaopa Yehova ndi mantha akulu, namphera Yehova nsembe, nawinda. 17#Mat. 12.40; Luk. 11.30Koma Yehova anaikiratu chinsomba chachikulu chimeze Yona; ndipo Yona anali m'mimba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku.

Currently Selected:

YONA 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in