YouVersion Logo
Search Icon

YONA 2

2
Pemphero la Yona ali m'mimba mwa chinsomba
1Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake ali m'mimba mwa nsombayo. 2#Mas. 120.1Ndipo anati,
Ndinaitana Yehova m'nsautso yanga,
ndipo anandiyankha ine;
ndinafuula ndili m'mimba ya manda,
ndipo munamva mau anga.
3 # Mas. 42.7; 88.6 Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja,
ndipo madzi anandizinga;
mafunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.
4Ndipo ndinati, Ndatayika ndichoke pamaso panu;
koma ndidzapenyanso Kachisi wanu wopatulika.
5 # Mas. 69.1 Madzi anandizinga mpaka moyo wanga,
madzi akuya anandizungulira,
kayandeyande wa m'nyanja anandikulunga mutu.
6 # Mas. 16.10 Ndinatsikira kumatsinde a mapiri,
mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha;
koma munandikwezera moyo wanga
kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga.
7 # Mas. 18.6 Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukira Yehova;
ndi pemphero langa linafikira Inu m'Kachisi wanu wopatulika.
8Iwo osamalira mabodza opanda pake
ataya chifundo chaochao.
9 # Mas. 3.8; 116.17-18 Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika,
ndidzakwaniritsa chowinda changa.
Chipulumutso ncha Yehova.
10Pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inamsanzira Yona kumtunda.

Currently Selected:

YONA 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in