YOHANE 14
14
Yesu aneneratu za kubweranso kwake
(1Ate. 4.14-17)
1Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso. 2#Yoh. 13.33, 36M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. 3#Mac. 1.11; Yoh. 17.24Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso. 4Ndipo kumene ndinkako Ine, mudziwa njira yake. 5Tomasi ananena ndi Iye, Ambuye, sitidziwa kumene munkako; tidziwa njira bwanji? 6#Aheb. 10.20; Yoh. 1.4, 17; 10.9Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.
Yesu ndi Atate ndiwo amodzi
7 #
Yoh. 8.19
Mukadazindikira Ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira Iye, ndipo mwamuona Iye. 8Filipo ananena ndi Iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo chitikwanira. 9#Akol. 1.15Yesu ananena naye, Kodi ndili ndi inu nthawi yaikulu yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate? 10#Yoh. 10.37-38Sukhulupirira kodi kuti ndili Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine achita ntchito zake. 11#Yoh. 7.16Khulupirirani Ine, kuti Ine ndili mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati si chomwecho, khulupirirani Ine chifukwa cha ntchito zomwe. 12#Mat. 21.21-22Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita Ine kwa Atate. 13#Mat. 21.21-22Ndipo chimene chilichonse mukafunse m'dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana. 14Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzachita. 15#Yoh. 14.21, 23Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.
Lonjezo la Mzimu Woyera
16 #
Yoh. 15.26; 16.13 Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu kunthawi yonse, 17#Yoh. 15.26; 16.13; 1Yoh. 2.27ndiye Mzimu wa choonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona Iye, kapena kumzindikira Iye. Inu mumzindikira Iye; chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu. 18#Mat. 28.20Sindidzakusiyani inu mukhale ana amasiye; ndidza kwa inu. 19#1Ako. 15.20Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndili ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo. 20#Yoh. 14.10Tsiku lomwelo mudzazindikira kuti ndili Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu. 21#Yoh. 14.15, 23Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye. 22Yudasi, si Iskariote, ananena ndi Iye, Ambuye, chachitika chiyani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi? 23#Yoh. 14.15; Chiv. 3.20Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo. 24#Yoh. 7.16Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine.
25Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu. 26#Luk. 24.49; Yoh. 14.16; 16.13Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.
Mphatso ya mtendere
27 #
Yoh. 14.1; Afi. 4.7 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha. 28#Yoh. 10.29-30; 14.3, 18Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu ndi Ine. 29#Yoh. 16.4Ndipo tsopano ndakuuzani chisanachitike, kuti pamene chitachitika mukakhulupirire. 30#Yoh. 12.31Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine; 31#Afi. 2.8koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate, ndi kuti ndichita monga momwe Atate wandilamula. Nyamukani, tizimuka kuchokera kuno.
Currently Selected:
YOHANE 14: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi