YOHANE 13
13
Yesu asambitsa mapazi a anyamata ake
1 #
Yoh. 12.23
Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro. 2#Luk. 22.3Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye, 3#Mat. 11.27; Yoh. 8.42Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa Iye zonse m'manja mwake, ndi kuti anachokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu, 4#Luk. 22.27ananyamuka pamgonero, navula malaya ake; ndipo m'mene adatenga chopukutira, anadzimanga m'chuuno. 5Pomwepo anathira madzi m'nsambidwe, nayamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira, chimene anadzimanga nacho. 6#Mat. 3.14Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi Iye, Ambuye, kodi Inu mundisambitsa ine mapazi? 7#Yoh. 13.12-14Yesu anayankha nati kwa iye, Chimene ndichita Ine suchidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwake. 8#Aef. 5.26Petro ananena ndi Iye, Simudzasambitsa mapazi anga kunthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe cholandira pamodzi ndi Ine. 9Simoni Petro ananena ndi Iye, Ambuye, si mapazi anga okha, komanso manja ndi mutu. 10#Yoh. 15.3Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai. 11#Yoh. 6.64Pakuti anadziwa amene adzampereka Iye; chifukwa cha ichi anati, Simuli oyera nonse.
12Pamenepo, atatha Iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ake, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi? 13#Mat. 23.8, 10Inu munditcha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene. 14#Aro. 12.10; Agal. 6.1-2Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake. 15Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite. 16#Mat. 10.24Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake; kapena mtumwi sali wamkulu ndi womtuma iye. 17#Yak. 1.22, 25Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzichita. 18#Mas. 41.9Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake. 19Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene. 20#Mat. 10.40Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wolandira amene aliyense ndimtuma, andilandira Ine; koma wolandira Ine alandira wondituma Ine.
Yesu aneneratu kuti Yudasi adzampereka
(Mat. 26.20-25; Mrk. 14.17-21)
21 #
Mat. 26.21
Yesu m'mene adanena izi, anavutika mumzimu, nachita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine. 22Ophunzira analikupenyana wina kwa mnzake, ndi kusinkhasinkha kuti ananena za yani. 23#Yoh. 19.26Koma mmodzi wa ophunzira ake, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa chifuwa cha Yesu. 24Pamenepo Simoni Petro anamkodola nanena naye, Utiuze ndiye yani amene anena za iye. 25Iyeyu potsamira pomwepo, pa chifukwa cha Yesu, anena ndi Iye, Ambuye, ndiye yani? 26Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa. Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote. 27#Luk. 22.3Ndipo pambuyo pake pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Chimene uchita, chita msanga. 28Koma palibe mmodzi wa iwo akuseamako anadziwa chimene anafuna, poti atere naye. 29#Yoh. 12.6Pakuti popeza Yudasi anali nalo thumba, ena analikuyesa kuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa pachikondwerero; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi. 30Pamenepo iyeyo m'mene adalandira nthongo, anatuluka pomwepo. Koma kunali usiku.
31 #
Yoh. 12.23; 14.13 Tsono m'mene adatuluka, Yesu ananena, Tsopano walemekezeka Mwana wa Munthu, ndipo Mulungu walemekezedwa mwa Iye; 32#Yoh. 17.1, 4-6ndipo Mulungu adzamlemekeza Iye mwa Iye yekha, adzamlemekeza Iye tsopano apa. 33#Yoh. 7.34Tiana, katsala kanthawi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndinkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano. 34#Lev. 19.18; Yoh. 15.12, 17; 1Yoh. 2.7-8Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. 35#1Yoh. 4.20Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli ophunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.
Yesu aneneratu kuti Petro adzamkana
(Mat. 26.33-35; Mrk. 14.29-31; Luk. 22.33-34)
36 #
Yoh. 21.18, 22 Simoni Petro anena ndi Iye, Ambuye, mumuka kuti? Yesu anayankha, Kumene ndimukako sungathe kunditsata Ine tsopano; koma, udzanditsata bwino lomwe. 37#Mat. 26.33-35Petro ananena ndi Iye, Ambuye, sindingathe kukutsatani Inu tsopano chifukwa ninji? Ndidzataya moyo wanga chifukwa cha Inu. 38Yesu anayankha, Moyo wako kodi udzautaya chifukwa cha Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asanalire tambala udzandikana Ine katatu.
Currently Selected:
YOHANE 13: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi