YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 42

42
Yeremiya achenjeza anthu asapite ku Ejipito
1Ndipo akazembe onse a nkhondo, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi Yezaniya mwana wake wa Hosaya, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono, kufikira wamkulu, anayandikira, 2#1Sam. 7.8nati kwa Yeremiya mneneri, Chipembedzero chathu chigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Ambuye Mulungu wanu, chifukwa cha otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife; 3#Yes. 26.7; Mat. 7.14kuti Yehova Mulungu wanu atisonyeze ife njira imene tiyendemo, ndi chomwe tichite. 4#1Maf. 22.14Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti chilichonse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu. 5#Gen. 31.48, 50Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati sitichita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife. 6#Deut. 6.3Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.
7Ndipo panali atapita masiku khumi, mau a Yehova anadza kwa Yeremiya. 8Ndipo anaitana Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu, 9nati kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, kwa Iye amene munandituma ine ndigwetse pembedzero lanu pamaso pake, 10#Deut. 32.36Ngati mudzakhalabe m'dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa nacho chisoni choipa chimene ndakuchitirani inu. 11#Yes. 43.5; Aro. 8.31Musaope mfumu ya ku Babiloni, amene mumuopa; musamuope, ati Yehova: pakuti Ine ndili ndi inu kukupulumutsani, ndi kukulanditsani m'dzanja lake. 12#Neh. 1.11Ndipo ndidzakuchitirani inu chifundo, kuti iye akuchitireni inu chifundo, nakubwezereni inu kudziko lanu. 13#Yer. 44.16Koma mukati, Sitidzakhala m'dziko muno; osamvera mau a Yehova Mulungu wanu; 14ndi kuti, Iai; tidzanka ku Ejipito, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala; 15chifukwa chake mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe m'Ejipito, kukakhala m'menemo; 16#Ezk. 11.8pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m'menemo m'dziko la Ejipito, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Ejipito; pamenepo mudzafa. 17#Yer. 44.14Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Ejipito kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku choipa chimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense. 18#Yer. 7.20Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala m'Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa m'Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano. 19#Deut. 17.6Yehova wanena za inu, otsala inu a Yuda, Musalowe m'Ejipito; mudziwetu kuti ndakulangizani inu lero. 20#Yer. 42.2Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzachita. 21Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamva mau a Yehova Mulungu wanu m'chinthu chilichonse chimene Iye wanditumira ine nacho kwa inu. 22#Yer. 42.16-17Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi chaola, komwe mufuna kukakhalako.

Currently Selected:

YEREMIYA 42: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 42