YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 4

4
1 # Yer. 3.1, 22 Ngati udzabwera, Israele, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzachotsa zonyansa zako pamaso panga sudzachotsedwa. 2#Gen. 22.18; Agal. 3.8Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.
Adani achilendo adzagwera dziko la Yuda
3 # Hos. 10.12; Mat. 13.7, 22 Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga. 4#Aro. 2.28, 29; Akol. 2.11Mudzidulire nokha kwa Yehova, chotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala m'Yerusalemu; ukali wanga ungatuluke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe anu. 5Nenani m'Yuda, lalikirani m'Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'midzi ya malinga. 6#Yer. 1.13-15Kwezani mbendera kuyang'ana ku Ziyoni; thawani kuti mupulumuke, musakhale; pakuti ndidza ndi choipa chochokera kumpoto ndi kuononga kwakukulu. 7#2Maf. 24.1Mkango wakwera kutuluka m'nkhalango mwake, ndipo woononga amitundu ali panjira, watuluka m'mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti midzi yako ipasuke mulibenso wokhalamo. 8#Yes. 22.12Pamenepo, valani chiguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wa kuopsa wa Yehova sunabwerera pa ife. 9Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, kuti mtima wa mfumu udzataika, ndi mitima ya akulu; ndipo ansembe adzazizwa, ndi aneneri adzadabwa. 10#Ezk. 14.9; 2Ate. 2.11Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! Ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo. 11Pa nthawi yomweyo adzati kwa anthu awa ndi kwa Yerusalemu, Mphepo yotentha yochokera kumapiri oti see m'chipululu yopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga, yosapetera, yosayeretsa; 12mphepo yolimba yochokera kumeneko idzandifika ine; tsopanonso ndidzaweruza iwo maweruzo. 13#Yes. 5.28Taonani, adzadza ngati mitambo, ndi magaleta ake ngati kamvulumvulu; akavalo ake athamanga kopambana mphungu. Tsoka ife! Pakuti tapasuka. 14#Yak. 4.8Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati? 15Pakuti mau anena m'Dani nalalikira nsautso m'phiri la Efuremu: 16Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira kudziko lakutali, nainenera midzi ya Yuda mau ao. 17#2Maf. 25.1, 4Monga adindo a m'munda amzinga iye; chifukwa andipandukira Ine, ati Yehova. 18#Mas. 107.17Njira yako ndi ntchito zako zinakuchitira izi; ichi ndicho choipa chako ndithu; chili chowawa ndithu, chifikira kumtima wako.
19 # Yes. 22.4; Luk. 19.42 Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo. 20Alalikira chipasuko chilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsalu zanga zotchinga m'kamphindi. 21Kufikira liti ndidzaona mbendera, ndi kumva kulira kwa lipenga? 22#Aro. 16.19Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.
23 # Gen. 1.2 Ndinaona dziko lapansi, ndipo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika. 24Ndinaona mapiri, taona ananthunthumira; ndipo zitunda zonse zinagwedezeka. 25Ndinaona, ndipo taona, panalibe munthu, ndi mbalame zonse zakumwamba zinathawa. 26Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali chipululu, ndipo midzi yake yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wake woopsa. 27#Neh. 9.31; Yer. 5.10Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa. 28#Num. 23.19; Hos. 4.1-3Chifukwa chimenecho dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; chifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo. 29Mudzi wonse uthawa m'phokoso la apakavalo ndi amauta; adzalowa m'nkhalango, adzakwera pamiyala; midzi yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu m'menemo. 30#2Maf. 9.30Nanga iwe, udzachita chiyani pamene udzafunkhidwa? Ngakhale udziveka ndi zofiira, ngakhale udziveka ndi zokometsera zagolide, ngakhale udzikuzira maso ako ndi kupaka, udzikometsera pachabe; mabwenzi adzakunyoza adzafuna moyo wako. 31Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.

Currently Selected:

YEREMIYA 4: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy