Ngati udzabwera, Israele, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzachotsa zonyansa zako pamaso panga sudzachotsedwa. Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.