YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 38

38
Yeremiya aponyedwa m'dzenje muli thope
1Ndipo Sefatiya mwana wa Matani ndi Gedaliya mwana wa Pusuri, ndi Yukala mwana wa Selemiya, ndi Pasuri mwana wa Malikiya, anamva mau amene Yeremiya ananena ndi anthu onse, kuti, 2#Yer. 21.9Yehova atero, Iye wakukhala m'mudziwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; koma iye wakutulukira kunka kwa Ababiloni adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wake ngati chofunkha, nadzakhala ndi moyo. 3#Yer. 21.10Yehova atero, Mudziwu udzapatsidwatu m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda. 4#Yes. 26.11Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mudzi uno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao. 5Ndipo mfumu Zedekiya anati, Taonani, ali m'manja mwanu; pakuti mfumu singathe kuchita kanthu kotsutsana nanu. 6#Yer. 37.21Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo. 7#Yer. 39.16Ndipo pamene Ebedemeleki Mkusi, mdindo, anamva kuti anamuika Yeremiya m'dzenje; mfumu ilikukhala pa chipata cha Benjamini; 8Ebedemeleki anatuluka m'nyumba ya mfumu, nanena ndi mfumu, kuti, 9Mbuyanga mfumu, anthu awa anachita zoipa m'zonse anachitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo chifukwa cha njala; pakuti mulibe chakudya china m'mudzimu. 10Ndipo mfumu inamuuza Ebedemeleki Mkusi, kuti, Tenga anthu makumi atatu, umkweze numtulutse Yeremiya mneneri m'dzenjemo, asanafe. 11Ndipo Ebedemeleki anatenga anthuwo, nalowa nao m'nyumba ya mfumu ya pansi pa nyumba ya chuma, natenga m'menemo nsalu zakale zotaya ndi zansanza zovunda, nazitsitsira ndi zingwe kwa Yeremiya m'dzenjemo. 12Ndipo Ebedemeleki Mkusi anati kwa Yeremiya, Kulungatu zingwe ndi nsaluzi zotaya zakale ndi zansanza ndi kuzikwapatira. Ndipo Yeremiya anachita chomwecho. 13#Yer. 37.21Ndipo anamkweza Yeremiya ndi zingwe, namtulutsa m'dzenjemo; ndipo Yeremiya anakhalabe m'bwalo la kaidi.
14Ndipo mfumu Zedekiya anatuma, namtenga Yeremiya mneneri nalowa naye m'khomo lachitatu la nyumba ya Yehova; ndipo mfumu inati kwa Yeremiya, Ndidzakufunsa iwe kanthu; usandibisire ine kanthu. 15Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Ndikakufotokozerani, kodi simudzandipha ine? Ndipo ndikakupangirani, simudzandimvera ine. 16#Yes. 57.16Ndipo mfumu Zedekiya analumbira m'tseri kwa Yeremiya, kuti, Pali Yehova, amene anatilengera ife moyo uno, sindidzakupha iwe sindidzakupereka iwe m'manja mwa anthu awa amene afuna moyo wako. 17Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Ngati mudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mudziwu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu; 18koma ngati simudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudziwu udzaperekedwa m'dzanja la Ababiloni, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao. 19#1Sam. 31.4Ndipo mfumu Zedekiya anati kwa Yeremiya, Ine ndiopa Ayuda amene anandipandukira ine kunka kwa Ababiloni, angandipereke ine m'manja mwao, angandiseke. 20Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, chomwecho kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe. 21Koma ngati mukana kutuluka, mau anandisonyeza Yehova ndi awa: 22Taonani, akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya Yuda adzatulutsidwa kunka kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m'thope, abwerera m'mbuyo. 23#Yer. 39.6Ndipo adzatulutsira Ababiloni akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m'manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babiloni; ndipo mudzatenthetsa mudziwu ndi moto. 24Ndipo Zedekiya anati kwa Yeremiya, Anthu asadziwe mau amene, ndipo sudzafa. 25Koma akamva akulu kuti ndalankhula ndi iwe, nakafika kwa iwe, ndi kuti kwa iwe, Utifotokozere ife chomwe wanena kwa mfumu; osatibisira ichi, ndipo sitidzakupha iwe; ndiponso zomwe mfumu inanena kwa iwe; 26#Yer. 37.20pamenepo uziti kwa iwo, Ndinagwa ndi pembedzero langa pamaso pa mfumu, kuti asandibwezerenso kunyumba ya Yonatani ndifere komweko. 27Ndipo akulu onse anadza kwa Yeremiya, namfunsa; ndipo iye ananena nao monga mwa mau onsewo anamuuza mfumu. Ndipo analeka kunena naye; pakuti sikunamveka mlandu. 28#Yer. 38.13Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi mpaka tsiku lakugwidwa Yerusalemu. Ndipo anali komweko pogwidwa Yerusalemu.

Currently Selected:

YEREMIYA 38: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 38