YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 37

37
Yeremiya m'kaidi
1 # 2Maf. 24.17 Ndipo Zedekiya mwana wa Yosiya anakhala mfumu m'malo a Koniya mwana wa Yehoyakimu, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni inamlowetsa mfumu m'dziko la Yuda. 2#2Mbi. 36.12, 14Koma ngakhale iye, ngakhale atumiki ake, ngakhale anthu a padziko, sanamvere mau a Yehova, amene ananena mwa Yeremiya mneneri.
3 # Yer. 52.24 Ndipo Zedekiya mfumu anatuma Yehukala mwana wa Selemiya, ndi Zefaniya mwana wa Maaseiya wansembe, kwa Yeremiya mneneri, kukanena, Mutipemphereretu kwa Yehova Mulungu wathu. 4Ndipo Yeremiya analikuyendayenda mwa anthu; chifukwa asanamuike iye m'nyumba yandende. 5#Ezk. 17.15Ndipo nkhondo ya Farao inatuluka m'Ejipito; ndipo pamene Ababiloni omangira misasa Yerusalemu anamva mbiri yao, anachoka ku Yerusalemu. 6Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya mneneri, kuti, 7#2Maf. 24.7Atero Yehova, Mulungu wa Israele: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakutulukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Ejipito ku dziko lao. 8#Yer. 34.22Ndipo Ababiloni adzabweranso, nadzamenyana ndi mudzi uwu; ndipo adzaulanda, nadzautentha ndi moto. 9Yehova atero: Musadzinyenge, kuti, Ababiloni adzatichokera ndithu; pakuti sadzachoka. 10Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Ababiloni akumenyana nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okhaokha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m'hema wake ndi kutentha mudzi uwu ndi moto.
11 # Yer. 37.5 Ndipo panali pamene nkhondo ya Ababiloni inachoka ku Yerusalemu chifukwa cha nkhondo ya Farao, 12#Yer. 32.7-11pamenepo Yeremiya anatuluka m'Yerusalemu kumuka kudziko la Benjamini, kukalandira gawo lake kumeneko. 13Pokhala iye m'chipinda cha Benjamini, kapitao wa alonda anali kumeneko, dzina lake Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya; ndipo iye anamgwira Yeremiya mneneri, nati, Ulinkupandukira kwa Ababiloni. 14Ndipo anati Yeremiya, Kunama kumeneko; ine sindipandukira kwa Ababiloni; koma sanamvere iye; ndipo Iriya anamgwira Yeremiya, nanka naye kwa akulu. 15#Yer. 38.26Ndipo akulu anakwiyira Yeremiya, nampanda iye, namuika m'nyumba yandende m'nyumba ya Yonatani mlembi; pakuti anaiyesa ndende. 16#Yer. 38.6Atafika Yeremiya kunyumba yadzenje, ku tizipinda take nakhalako Yeremiya masiku ambiri; 17pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwake, niti, Kodi alipo mau ochokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo. Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni. 18Ndipo Yeremiya anati kwa mfumu Zedekiya, Ndachimwira inu chiyani, kapena atumiki anu, kapena anthu awa, kuti mwandiika m'nyumba yandende? 19Tsopano ali kuti aneneri anu, amene ananenera inu, kuti, Mfumu ya ku Babiloni sidzakudzerani inu, kapena dziko lino? 20Tsopano tamvanitu, mbuyanga mfumu; pembedzero langa ligwe pamaso panu; kuti musandibwezere kunyumba ya Yonatani mlembi, ndingafe kumeneko. 21#Yer. 32.2; 38.13Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m'bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma kumseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m'mudzi. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi.

Currently Selected:

YEREMIYA 37: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 37