YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 2

2
Yehova adzudzula anthu a Israele
1Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, nati, 2#Deut. 2.7Pita nufuule m'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, chikondi cha matomedwe ako; muja unanditsata m'chipululu m'dziko losabzalamo. 3#Eks. 19.5-6; Yak. 1.18Israele anali wopatulikira Yehova, zipatso zoundukula za zopindula zake; onse amene adzamudya iye adzayesedwa opalamula; choipa chidzawagwera, ati Yehova.
4Tamvani mau a Yehova, iwe nyumba ya Yakobo, ndi inu mabanja onse a nyumba ya Israele; 5#Mik. 6.3atero Yehova, Atate anu apeza chosalungama chanji mwa Ine, kuti andichokera kunka kutali, natsata zachabe, nasanduka achabe? 6#Yes. 63.11-13Osati Ali kuti Yehova amene anatikweza kuchokera kudziko la Ejipito, natitsogolera m'chipululu, m'dziko loti see ndi la maenje, m'dziko la chilala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitanso anthu, losamangamo anthu? 7#Num. 13.27; 35.33-34Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zake, ndi zabwino zake; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa cholandira changa chonyansa. 8#Yer. 23.13; Mala. 2.6-7Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? Ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula. 9#Ezk. 20.35-36Chifukwa chake ndidzatsutsananso nanu, ati Yehova, ndi ana a ana anu ndidzatsutsana nao. 10Pakuti pitani ku zisumbu za Kitimu nimuone; tumizani ku Kedara nimulingalire bwino; nimuone ngati chinalipo chotere. 11#Mas. 106.20; Aro. 1.23Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula. 12Muzizwe pamenepo, miyamba inu, muope kwambiri, mukhale ouma, ati Yehova. 13#Mas. 36.9; Yoh. 4.14Pakuti anthu anga anachita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong'aluka, zosakhalamo madzi. 14Kodi Israele ndi mtumiki? Kodi ndiye kapolo wobadwa m'nyumba? Afunkhidwa bwanji? 15Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lake, midzi yake yatenthedwa, mulibenso wokhalamo. 16Ananso a Nofi ndi a Tapanesi, anaswa pakati pamtu pako. 17#Yer. 4.18Kodi sunadzichitira ichi iwe wekha popeza unasiya Yehova Mulungu wako, pamene anatsogolera iwe panjira? 18#Yes. 30.1-2Tsopano uli nacho chiyani m'njira ya ku Ejipito, kumwa madzi a Sihori? Uli nacho chiyani m'njira ya ku Asiriya, kumwa madzi a m'mtsinje? 19#Hos. 5.5Choipa chako dzidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Yehova Mulungu wa makamu. 20#1Sam. 12.10Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama. 21#Yes. 5.1-7; Mat. 21.33Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo? 22#Hos. 13.12Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu. 23#Miy. 30.12Bwanji uti, Sindinaipitsidwa, sindinatsata Abaala? Ona njira yako m'chigwa, dziwa chimene wachichita; ndiwe ngamira yothamanga yoyenda m'njira zake; 24mbidzi yozolowera m'chipululu, yopumira mphepo pakufuna pake; pokomana nayo ndani adzaibweza? Onse amene aifuna sadzadzilemetsa; adzaipeza m'mwezi wake. 25#Yer. 18.12Kaniza phazi lako lisakhale losavala nsapato, ndi m'mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe chiyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao. 26Monga mbala ili ndi manyazi pamene igwidwa, chomwecho nyumba ya Israele ili ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, ndi aneneri ao; 27#Ower. 10.10amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kuvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni. 28#Yer. 11.12-13Koma ili kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kuvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa midzi yako, Yuda iwe.
29Chifukwa chanji mudzatsutsana ndi Ine nonse? Mwandilakwira Ine, ati Yehova. 30#Yes. 9.13Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga. 31Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israele chipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Chifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu? 32#Mas. 106.21; Hos. 8.14Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwitibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka. 33Kodi sukonzadi njira yako kufunafuna chilakolako? Chifukwa chake waphunzitsa akazi oipa njira zako. 34Ndiponso m'nsalu zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osachimwa; sunawapeza pakuboola, koma ponsepo. 35#Miy. 30.12; 1Yoh. 1.8, 10Koma unati, Ndili wosachimwa ndithu; mkwiyo wake wachoka pa ine. Taona, ndidzakuweruza iwe, chifukwa uti, Sindinachimwa. 36Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? Udzachitanso manyazi ndi Ejipito monga unachita manyazi ndi Asiriya. 37#2Sam. 13.19Koma udzatuluka kwa iyenso, manja ako pamtu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo.

Currently Selected:

YEREMIYA 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 2