OWERUZA 6
6
Midiyani agonjetsa Aisraele
1Koma ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Midiyani zaka zisanu ndi ziwiri. 2#Aheb. 11.38Pamene dzanja la Midiyani linalaka Israele, ana a Israele anadzikonzera ming'ang'ala ya m'mapiri, ndi mapanga, ndi malinga chifukwa cha Midiyani. 3Ndipo kunali, akabzala Israele, amakwera Amidiyani, ndi Amaleke, ndi ana a kum'mawa, inde amawakwerera; 4nawamangira misasa, namaononga zipatso za m'dziko mpaka ufika ku Gaza, osawasiyira chochirira njala m'Israele, ngakhale nkhosa, kapena ng'ombe, kapena bulu. 5Pakuti anakwera nazo zoweta zao ndi mahema ao, analowa ngati dzombe kuchuluka kwao; iwowa ndi ngamira zao zomwe nzosawerengeka; ndipo analowa m'dziko kuliononga. 6#Hos. 5.15Ndipo Israele anafooka kwambiri chifukwa cha Midiyani; ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova.
7Ndipo kunali, pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova chifukwa cha Midiyani, 8Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israele, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ine ndinakukwezani kuchokera m'Ejipito, ndi kukutulutsani m'nyumba ya ukapolo; 9ndipo ndinakulanditsani m'dzanja la Aejipito, ndi m'dzanja la onse akupsinja inu, ndi kuwaingitsa pamaso panu, ndi kukupatsani dziko lao; 10ndipo ndinati kwa inu, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musamaopa milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma simunamvera mau anga.
Mngelo wa Mulungu amdzera Gideoni
11 #
Aheb. 11.32
Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala m'Ofura, wa Yowasi Mwabiyezere; ndi mwana wake Gideoni analikuomba tirigu m'mopondera mphesa, awabisire Amidiyani. 12#Mac. 10.3Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera, nati kwa iye, Yehova ali nawe, ngwazi iwe, wamphamvu iwe. 13#Mas. 89.49Ndipo Gideoni ananena naye, Mbuye wanga, ngati Yehova ali nafe chatigwera ife bwanji chonsechi? Ndipo zili kuti zodabwitsa zake zonse zimene makolo athu anatiwerengera, ndi kuti, Sanatikweze kodi Yehova kuchokera m'Ejipito? Koma tsopano Yehova watitaya natipereka m'dzanja la Midiyani. 14#Aheb. 11.34Pamenepo Yehova anamtembenukira, nati, Muka nayo mphamvu yako iyi, nupulumutse Israele m'dzanja la Midiyani. Sindinakutuma ndi Ine kodi? 15#Eks. 3.11; 1Sam. 18.18Ndipo anati kwa Iye, Ha! Mbuye, ndidzapulumutsa Israele ndi chiyani? Taonani, banja langa lili loluluka m'Manase, ndipo ine ndine wamng'ono m'nyumba ya atate wanga. 16#Eks. 3.12Ndipo Yehova ananena naye, Popeza Ine ndidzakhala nawe udzakantha Amidiyani ngati munthu mmodzi. 17#Eks. 4.1-8Ndipo anati kwa Iye, Ngati mundikomera mtima mundionetse chizindikiro tsopano chakuti ndi Inu wakunena nane. 18#Gen. 18.3-8Musachoke pano, ndikupemphani, mpaka ndikudzerani ndi kutulutsa chopereka changa ndi kuchiika pamaso panu. Ndipo anati, Ndidzalinda mpaka ubwera. 19Ndipo Gideoni analowa, nakonza kambuzi ndi mikate yopanda chotupitsa ya efa wa ufa; nyamayi anaiika m'lichero, ndi msuzi anauthira mumbale, natuluka nazo kwa Iye ali patsinde pa thundu, nazipereka. 20Koma mthenga wa Mulungu ananena naye, Tenga nyamayi ndi mikate yopanda chotupitsa ndi kuziika pathanthwe pano ndi kutsanula msuzi. Ndipo anatero. 21#1Maf. 18.38Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m'dzanja lake, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo unatuluka moto m'thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda chotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pake. 22#Eks. 33.20Pamenepo Gideoni anaona kuti ndiye mthenga wa Yehova, nati Gideoni, Tsoka ine, Yehova Mulungu! Popeza ndaona mthenga wa Yehova maso ndi maso. 23#Dan. 10.19Ndipo Yehova anati kwa iye, Mtendere ukhale ndi iwe, usaope, sudzafa. 24Pamenepo Gideoni anammangira Yehova guwa la nsembe pomwepo; nalitcha Yehova-ndiye-mtendere; likali m'Ofura wa Aabiyezere ndi pano pomwe.
Gideoni agamula guwa la nsembe la Baala
25 #
Eks. 34.13
Ndipo kunali, usiku womwe uja Yehova ananena naye, Tenga ng'ombe ya atate wako, ndiyo ng'ombe yachiwiri ya zaka zisanu ndi ziwiri, nugamule guwa la nsembe la Baala ndilo la atate wako, nulikhe chifanizo chili pomwepo; 26numangire Yehova Mulungu wako guwa la nsembe pamwamba pa lingali, monga kuyenera; nutenge ng'ombe yachiwiriyo, nufukize nsembe yopsereza; nkhuni zake uyese chifanizo walikhacho. 27Pamenepo Gideoni anatenga amuna khumi mwa anyamata ake, nachita monga Yehova adanena naye; ndipo kunali, popeza anaopa akunyumba ya atate wake, ndi amuna akumudziwo, sanachichite msana, koma usiku. 28Ndipo pakuuka mamawa amuna akumudziwo, taonani, guwa la nsembe la Baala litagamuka, ndi chifanizo chinali pomwepo chitalikhidwa ndi ng'ombe yachiwiri yoperekedwa pa guwa la nsembe adalimanga. 29Nanenana wina ndi mnzake, Wachita ichi ndani? Ndipo atafunafuna nafunsafunsa, anati, Gideoni, mwana wa Yowasi wachita ichi. 30Pamenepo amuna akumudziwo anati kwa Yowasi, Umtulutse mwana wako kuti afe; pakuti anagamula guwa la nsembe la Baala, pakutinso analikha chifanizo chinali pomwepo. 31Koma Yowasi anati kwa onse akumuimirira, Kodi inu mumnenera Baala mlandu? Kapena kodi mudzampulumutsa iye? Iye amene amnenera mlandu aphedwe kukali m'mawa; akakhala mulungu adzinenere yekha mlandu, popeza wina wamgamulira guwa lake la nsembe. 32Chifukwa chake anamutcha tsiku lija Yerubaala, ndi kuti, Amnenere mlandu Baala popeza anamgamulira guwa lake la nsembe.
33Pamenepo Amidiyani onse ndi Aamaleke ndi ana a kum'mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m'chigwa cha Yezireele. 34Koma mzimu wa Yehova unavala Gideoni; naomba lipenga iye, ndi a banja la Abiyezere analalikidwa kumtsata iye. 35Ndipo anatuma mithenga kwa Manase konse; ndi iwonso analalikidwa kumtsata iye; natuma mithenga kwa Asere, ndi kwa Zebuloni, ndi kwa Nafutali; iwo nadzakomana nao. 36Ndipo Gideoni anati kwa Mulungu, Mukadzapulumutsa Israele ndi dzanja langa monga mwanena, 37taonani, ndidzaika chikopa cha ubweya popunthira tirigu; pakakhala mame pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pouma, pamenepo ndidzadziwa kuti mudzapulumutsa Israele ndi dzanja langa monga mwanena. 38Ndipo kunatero; pakuti anauka mamawa, nafinya chikopacho, nakamula mame a pachikopa, madzi ake odzala mbale. 39#Gen. 18.32Ndipo Gideoni ananena ndi Mulungu, Mkwiyo wanu usandiyakire, ndinene kamodzi kokha: ndikuyeseni kamodzi kokha ndi chikopa; paume pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pakhale mame. 40Ndipo Mulungu anatero usiku uja; pakuti panauma pachikopa pokha, ndi panthaka ponse panali mame.
Currently Selected:
OWERUZA 6: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi