OWERUZA 7
7
Gideoni apirikitsa nkhondo ya Amidiyani
1Pamenepo Yerubaala, ndiye Gideoni, ndi anthu onse okhala naye anauka mamawa, namanga misasa pa chitsime cha Harodi, ndi misasa ya Midiyani inali kumpoto kwao, pa phiri la More m'chigwa. 2#Deut. 8.17; Yes. 10.13; 1Ako. 1.29Ndipo Yehova anati kwa Gideoni. Anthu ali ndi iwe andichulukira kuti ndipereke Midiyani m'dzanja lao; angadzitame Israele pa Ine, ndi kuti, Dzanja la ine mwini landipulumutsa. 3#Deut. 20.8Ndipo tsopano, kalalike m'makutu a anthu, ndi kuti, Aliyense wochita mantha, nanjenjemera, abwerere nachoke pa phiri la Giliyadi. Ndipo anabwererako anthu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, natsalako zikwi khumi.
4Ndipo Yehova ananena ndi Gideoni, Anthu akali ochuluka; tsikira nao kumadzi, ndipo ndidzakuyesera iwo komweko; ndipo kudzali kuti iye amene ndimnena kwa iwe, Uyo azimuka nawe, yemweyo azimuka nawe; koma aliyense ndimnena kwa iwe, Uyo asamuke nawe, yemweyo asamuke. 5Ndipo anatsikira nao anthu kumadzi; ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Aliyense akapiza madzi pa lilime lake, monga akhatira galu, ameneyo amuike pa yekha; momwemo aliyense agwada pakumwa. 6Ndi kuwerenga kwa iwo akukhatira, ndi kuika dzanja lao kukamwa kwao, ndiko mazana atatu; koma ena onse anagwada pakumwa madzi. 7#1Sam. 14.6Ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ndi anthu mazana atatu akukhatira ndidzakupulumutsani, ndi kupereka Amidiyani m'dzanja lako; koma amuke anthu awa onse, yense kumalo kwake. 8Pamenepo anthu anatenga kamba m'dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israele amuke, yense kuhema kwake; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midiyani inali kunsi kwake m'chigwa. 9#Gen. 46.2-3Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m'dzanja lako. 10Koma ngati uopa kutsika, utsike naye Pura mnyamata wako kumisasa; 11#Ower. 7.13-15nudzamva zonena iwo; utatero manja ako adzalimbikitsidwa kutsikira kumisasa. Pamenepo anatsikira ndi Pura mnyamata wake ku chilekezero cha anthu azida a m'misasa. 12Ndipo Amidiyani ndi Aamaleke ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'chigwa, kuchuluka kwao ngati dzombe; ndi ngamira zao zosawerengeka, kuchuluka kwao ngati mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. 13Ndipo pakufikako Gideoni, taonani, panali munthu analikufotokozera mnzake loto, nati, Taona, kulota ndinalota, ndipo tapenya, mtanda wa mkate wabarele unakunkhulirakunkhulira m'misasa ya Midiyani, nufika kuhema, numgunda nagwa, numpidigula kuti hema anakhala chigwere. 14Ndipo mnzake anayankha nati, Ichi si china konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yowasi, munthu wa Israele; Mulungu wapereka Midiyani ndi a m'misasa onse m'dzanja lake.
15Ndipo kunali, pakumva Gideoni kufotokozera kwa lotolo ndi tanthauzo lake, anadziwerama; nabwera ku misasa ya Israele nati, Taukani, pakuti Yehova wapereka a m'misasa a Midiyani m'dzanja lanu. 16Ndipo anagawa amuna mazana atatu akhale magulu atatu, napatsa malipenga m'manja a iwo onse, ndi mbiya zopanda kanthu, ndi miuni m'kati mwa mbiyazo. 17Ndipo ananena nao, Mundipenyerere ine, ndi kuchita momwemo; ndipo taonani, pakufika ine pa chilekezero cha misasa, kudzali, monga ndichita ine, momwemo muzichita inu. 18Pamene ndiomba lipenga, ine ndi onse okhala nane, inunso muziomba lipenga pozungulira ponse pa misasa, ndi kunena kuti, Yehova ndi Gideoni.
19Motero Gideoni ndi amuna zana anali naye anafikira ku chilekezero cha misasa poyambira ulonda wa pakati, atasintha alonda tsopano apa; ndipo anaomba malipenga, naphwanya mbiya zokhala m'manja mwao. 20Ndi magulu atatuwo anaomba malipenga, naswa mbiyazo, nagwira miuni ndi dzanja lao lamanzere, ndi malipenga m'dzanja lao lamanja kuwaomba; ndipo anafuula, Lupanga la Yehova ndi la Gideoni. 21#Eks. 14.13-14; 2Mbi. 20.17Ndipo anaima yense m'mbuto mwake pozungulira misasa; pamenepo anathamanga a m'misasa onse, nafuula, nathawa. 22#1Sam. 14.20Ndipo mazana atatuwa anaomba malipenga, ndipo Yehova anakanthanitsa yense mnzake ndi lupanga m'misasa monse; ndi a m'misasa anathawa mpaka ku Betesita ku Zerera, mpaka ku malire a Abele-Mehola pa Tabati. 23Pamenepo anthu a Israele analalikidwa kuchokera ku Nafutali, ndi ku Asere, ndi ku Manase yense, nalondola Amidiyani. 24#Yoh. 1.28Gideoni anatumanso mithenga ku mapiri onse a Efuremu ndi kuti, Tsikani, kukomana ndi Amidiyani ndi kutsekereza madooko asanafike iwowa, mpaka ku Betebara ndi Yordani. Potero amuna onse a Efuremu anasonkhana pamodzi natsekereza madooko mpaka ku Betebara, ndi Yordani. 25#Mas. 83.11Ndipo anagwira akalonga awiri a Midiyani, Orebu ndi Zeebu; namupha Orebu ku thanthwe la Orebu; ndi Zeebu anamupha ku choponderamo mphesa cha Zeebu, nalondola Amidiyani; ndipo anadza nayo mitu ya Orebu ndi Zeebu kwa Gideoni tsidya lija la Yordani.
Currently Selected:
OWERUZA 7: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi