YouVersion Logo
Search Icon

OWERUZA 13

13
Aisraele agonjera Afilisti; abadwa Samisoni
1 # Ower. 2.11-14 Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova; nawapereka Yehova m'dzanja la Afilisti zaka makumi anai.
2 # 1Sam. 1.2; Luk. 1.7 Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lake ndiye Manowa; ndi mkazi wake analibe mwana, sanabala. 3#Ower. 6.12; Luk. 1.11Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna. 4#Ower. 13.14; Num. 6.2-3; Luk. 1.15Chifukwa chake udzisamalire, usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chinthu chilichonse chodetsa; 5#Num. 6.2, 5; 1Sam. 1.11; 7.13pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israele m'dzanja la Afilisti. 6Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wake ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ake ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunsa uko achokera kapena sanandiuzenso dzina lake; 7koma anati kwa ine, Taona, udzaima, ndi kubala mwana wamwamuna; ndipo tsopano usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chilichonse chodetsa; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire mpaka tsiku la kufa kwake. 8Pamenepo Manowa anapembedza Yehova, nati, Yehova, ndikupemphani, atidzerenso munthu wa Mulungu mudamtumayo, natilangize icho tizichitira mwanayo akadzabadwa. 9Ndipo Mulungu anamvera mau a Manowa; ndi mthenga wa Mulungu anamdzeranso mkaziyo, pamene anali m'munda, mwamuna wake Manowa palibe. 10Ndipo mkaziyo anafulumira nathamanga, nauza mwamuna wake, nanena naye, Taona, wandionekera munthu anandidzerayo tsiku lija. 11Nanyamuka Manowa natsata mkazi wake, namdzera mwamuna uja, nanena naye, Kodi ndinu mwamuna uja munalankhula ndi mkaziyu? Ndipo anati, Ndine amene. 12#Luk. 1.66Nati Manowa, Achitike tsopano mau anu; koma makhalidwe ake a mwanayo ndi machitidwe ake adzatani? 13Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Zonse ndinazinena ndi mkazi azisamalire. 14#Ower. 13.4Chilichonse chichokera kumpesa asadyeko, asamwe vinyo kapena choledzeretsa, kapena kudya chilichonse chodetsa; zonse ndinamlamulira azisunge. 15#Gen. 18.5Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Tiloleni tikuchedwetseni kuti tikukonzereni mwanawambuzi. 16Koma mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Ungakhale undichedwetsa, sindidzadya mkate wako; ndipo ukakonza nsembe yopsereza, uziipereka kwa Yehova. Pakuti Manowa sanadziwe kuti ndiye mthenga wa Yehova. 17Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Dzina lanu ndani, kuti, atachitika mau anu, tikuchitireni ulemu. 18#Gen. 32.29; Yes. 9.6Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ufunsiranji dzina langa, popeza lili lodabwitsa? 19Pamenepo Manowa anatenga mwanawambuzi pamodzi ndi nsembe yaufa, nazipereka kwa Yehova pathanthwe; ndipo mthengayo anachita modabwitsa, ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere. 20#Lev. 9.24; 1Mbi. 21.16; Mat. 17.6Pakuti kunali, pakukwera lawi la moto pa guwa la nsembe kumwamba, mthenga wa Yehova anakwera m'lawi la pa guwalo; ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere; nagwa iwowa nkhope zao pansi. 21#Ower. 6.22Ndipo mthenga wa Yehova sanaonekerenso kwa Manowa kapena kwa mkazi wake. Pamenepo anadziwa Manowa kuti ndiye mthenga wa Yehova. 22#Gen. 32.30Nati Manowa kwa mkazi wake, Tidzafa ndithu pakuti taona Mulungu. 23Koma mkazi wake ananena naye, Yehova akadafuna kutipha, sakadalandira nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa pa dzanja lathu, kapena kutionetsa izi zonse, kapena kutimvetsa zoterezi nthawi yino. 24#1Sam. 2.26; Luk. 1.80; 2.52Ndipo mkaziyo anabala mwana wamwamuna namutcha dzina lake Samisoni; nakula mwanayo, Yehova namdalitsa. 25#1Sam. 11.6Ndipo mzimu wa Yehova unayamba kumfulumiza mtima ku misasa ya Dani pakati pa Zora ndi Esitaoli.

Currently Selected:

OWERUZA 13: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in