YouVersion Logo
Search Icon

EZARA 4

4
Asamariya aneneza Ayuda omanga Kachisi kwa Ahasuwero
1 # Ezr. 4.7-10 Atamva tsono adani a Yuda ndi Benjamini kuti ana aja a ndende analikumangira Yehova Mulungu wa Israele Kachisi, 2#2Maf. 17.24, 32-33anayandikira kwa Zerubabele, ndi kwa akulu a nyumba za makolo, nanena nao, Timange pamodzi nanu; pakuti timfuna Mulungu wanu monga inu, ndipo timamphera nsembe chiyambire masiku a Esarahadoni mfumu ya Asiriya, amene anatikweretsa kuno. 3#Ezr. 1.1-3; Neh. 2.20Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akulu otsala a nyumba za makolo a Israele, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi mfumu ya Persiya watilamulira. 4Pamenepo anthu a m'dziko anafoketsa manja a anthu Ayuda, nawavuta pomanga, 5nalembera opangira atsutsane nao, nafafanize uphungu wao, masiku onse a Kirusi mfumu ya Persiya, mpaka ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya. 6Ndipo pokhala mfumu Ahasuwero, poyambira ufumu wake, analembera chowaneneza okhala m'Yuda ndi m'Yerusalemu.
7Ndipo masiku a Arita-kisereksesi Bisilamu, Mitiredati, Tabeele, ndi anzao otsala, analembera kwa Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya; ndi chilembedwe chake cha kalatayo anamlemba m'Chiaramu, namsanduliza m'Chiaramu. 8Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, analemba kalata kwa mfumu Arita-kisereksesi, wakutsutsana naye Yerusalemu motere: 9nalembera Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, ndi anzake otsala; Adinai, ndi Afarisatikai, Ataripilai, Afarisai, Aereke, Ababiloni, Asusani, Adehai, Aelamu, 10ndi amitundu otsala amene, Osinapara wamkulu ndi womveka adawatenga mikoli, nawakhalitsa m'mudzi wa Samariya, ndi m'dziko lotsala tsidya lino la mtsinje wa Yufurate. 11Zolembedwa m'kalatayo ndizo: Kwa Arita-kisereksesi mfumu, ife akapolo anu, anthu a tsidya lino la mtsinjewo, tikupatsani moni. 12Adziwe mfumu kuti, Ayuda adakwerawo ochokera kwanu atifikira ife ku Yerusalemu, alikumanga mudzi uja wopanduka ndi woipa, alikutsiriza malinga ake, nalumikiza maziko ake. 13Adziwe tsono mfumu, kuti akamanga mudzi uwu ndi kutsiriza malinga ake, sadzapereka msonkho, kapena thangata, kapena msonkho wa m'njira; ndipo potsiriza pake kudzasowetsa mafumu. 14Popeza tsono timadya mchere wa m'nyumba ya mfumu, sitiyenera kungopenyerera mpepulo wa pa mfumu; chifukwa chake tatumiza ndi kudziwitsa mfumu, 15kuti afunefune m'buku la chikumbutso la makolo anu; momwemo mudzapeza m'buku la chikumbutso, ndi kudziwa kuti mudzi uwu ndi mudzi wopanduka, ndi wosowetsa mafumu, ndi maiko; ndi kuti amadziyendera m'menemo kuyambira kale lomwe; ndicho chifukwa chakuti anapasula mudzi uwu. 16Tili kudziwitsa mfumu kuti ukamangidwa mudziwu, nakatsirizidwa malinga ake, simudzakhala nalo gawo tsidya lino la mtsinjewo.
Mfumu iwaletsa asamange Kachisi
17Mfumu nibweza mau kwa Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi kwa Simisai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala m'Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Mtendere, ndi nthawi yakuti. 18Kalatayo mwatitumizira anandiwerengera momveka. 19Ndipo ndinalamulira anthu, nafunafuna, napeza kuti mudzi uwu unaukira mafumu kuyambira kale lomwe, ndi kuti akachitamo mpanduko ndi kudziyendera. 20#1Maf. 4.21Panalinso mafumu amphamvu m'Yerusalemu amene anachita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m'njira. 21Mulamulire tsono kuti anthu awa aleke, ndi kuti asamange mudzi uwu, mpaka ndidzalamulira ndine. 22Chenjerani mungadodomepo, chidzakuliranji chisauko cha kusowetsa mafumu? 23Pamenepo atawerenga malemba a kalata wa mfumu Arita-kisereksesi kwa Rehumu, ndi Simisai mlembi, ndi anzao, anafulumira kupita ku Yerusalemu kwa Ayuda, nawaletsa ndi dzanja lamphamvu. 24Momwemo inalekeka ntchito ya nyumba ya Mulungu yokhala ku Yerusalemu; nilekeka mpaka chaka chachiwiri cha ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya.

Currently Selected:

EZARA 4: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in