YouVersion Logo
Search Icon

EKSODO 6

6
1 # Eks. 12.31, 33 Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake.
2 # Yes. 42.8 Ndipo Mulungu ananena ndi Mose, nati kwa iye, Ine ndine YEHOVA: 3#Mas. 68.4; 83.18ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwika kwa iwo ndi dzina langa YEHOVA. 4#Gen. 17.4, 8Ndipo ndinakhazikitsanso nao chipangano changa, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m'mwemo. 5#Eks. 2.24Ndamvanso kubuula kwa ana a Israele, amene Aejipito awayesa akapolo; ndipo ndakumbukira chipangano changa. 6#2Maf. 17.36Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo akulu; 7#2Sam. 7.24ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakutulutsa inu pansi pa akatundu a Aejipito. 8#Gen. 26.3Ndipo ndidzakulowetsani m'dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isaki ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova. 9Ndipo Mose ananena chomwecho ndi ana a Israele; koma sanamvere Mose chifukwa cha kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera.
10Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, 11Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake. 12#Eks. 4.10; 6.30Koma Mose ananena pamaso pa Yehova, ndi kuti, Onani, ana a Israele sanandimvere ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula? 13Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israele, ndi za Farao mfumu ya Aejipito, kuti atulutse ana a Israele m'dziko la Ejipito.
Chibadwidwe cha Mose ndi Aroni
14 # Gen. 46.9 Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana amuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amene ndiwo mabanja a Rubeni. 15Ndi ana amuna a Simeoni ndiwo: Yemuwele, ndi Yamini, ndi Ohadi, Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo mwana wa mkazi wa Mkanani; amene ndiwo mabanja a Simeoni. 16Ndipo maina a ana amuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri. 17Ana amuna a Geresoni ndiwo: Libini ndi Simei, mwa mabanja ao. 18Ndi ana amuna a Kohati ndiwo: Amuramu ndi Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele; ndipo zaka za moyo wa Kohati ndizo zana limodzi ndi makumi atatu ndi kudza zitatu. 19Ndipo ana amuna a Merari ndiwo: Mali ndi Musi. Amenewo ndiwo mabanja a Levi mwa kubadwa kwao. 20Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri. 21Ndi ana amuna a Izihara ndiwo: Kora ndi Nefegi, ndi Zikiri. 22Ndi ana amuna a Uziyele ndiwo: Misaele, ndi Elizafani, ndi Sitiri. 23Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara. 24Ndipo ana amuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiyasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora. 25Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana akazi a Putiyele akhale mkazi wake, ndipo anambalira Finehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja ao. 26Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Tulutsani ana a Israele m'dziko la Ejipito mwa makamu ao. 27Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aejipito, awatulutse ana a Israele m'Ejipito; Mose ndi Aroni amenewa.
Mulungu ampangira Mose
28Ndipo kunali, tsiku limene Yehova ananena ndi Mose m'dziko la Ejipito, 29Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova; lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito zonsezi Ine ndizinena nawe. 30Koma Mose anati pamaso pa Yehova, Onani, ine ndili wa milomo yosadula ndipo Farao adzandimvera bwanji?

Currently Selected:

EKSODO 6: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in