YouVersion Logo
Search Icon

EKSODO 3

3
Kuitanidwa kwa Mose
1Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu. 2Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera m'chilangali chamoto chotuluka m'kati mwa chitsamba; ndipo anapenya, ndipo taonani, chitsamba chilikuyaka moto, koma chosanyeka chitsambacho. 3#Mac. 7.31Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone chooneka chachikulucho, chitsambacho sichinyeka bwanji. 4Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m'kati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndili pano. 5#Yos. 5.15; Mlal. 5.1Ndipo Iye anati, Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika. 6#Yes. 6.1-5; Mat. 22.32Ananenanso, Ine ndine Mulungu wa atate wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yake; popeza anaopa kuyang'ana Mulungu. 7#Mas. 106.44Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m'Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao; 8ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi. 9Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israele kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aejipito awapsinja nako. 10Tiye tsopano, ndikutuma kwa Farao, kuti utulutse anthu anga, ana a Israele m'Ejipito. 11#Yes. 6.5, 8; Yer. 1.6Koma Mose anati kwa Mulungu Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israele m'Ejipito? 12#Eks. 19.2; Yos. 1.5Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo m'Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano. 13Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israele, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? Ndikanena nao chiyani? 14#Aheb. 13.8Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu. 15#Mas. 135.13Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo. 16#Gen. 15.14, 16; 50.24Muka, nukasonkhanitse akulu a Israele, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuona chomwe akuchitirani m'Ejipito; 17ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m'mazunzo a Aejipito, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. 18Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu. 19Koma Ine ndidziwa kuti mfumu ya Aejipito siidzalola inu kumuka, inde lingakhale ndi dzanja lamphamvu ai. 20#Eks. 7.5Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aejipito ndi zozizwa zanga zonse ndizichita pakati pake; ndi pambuyo pake adzakulolani kumuka. 21Ndipo ndidzapatsa anthu awa ufulu pamaso pa anthu a Ejipito; ndipo kudzakhala, pamene mutuluka simudzatuluka opanda kanthu; 22#Eks. 11.2koma mkazi yense adzafunse mnzake, ndi mlendo wokhala m'nyumba mwake, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolide, ndi zovala; ndipo mudzaveke nazo ana anu aamuna ndi aakazi; ndipo mudzafunkhe za Aejipito.

Currently Selected:

EKSODO 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in