Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m'Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao; ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.