EKSODO 17
17
Madzi atuluka m'thanthwe ku Horebu
1Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona m'Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu. 2#Deut. 6.16; 1Ako. 10.9Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe. Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova? 3#Eks. 15.24Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu? 4#1Sam. 30.6; Luk. 13.34; Yoh. 8.59; Mac. 7.58Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Andilekera pang'ono kundiponya miyala. 5Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pita pamaso pa anthu, nutenge pamodzi nawe akulu ena a Israele; nutenge m'dzanja mwako ndodo ija unapanda nayo nyanja, numuke. 6#Mas. 114.8; 1Ako. 10.4Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe m'Horebu; ndipo upande thanthwe, nadzatulukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anachita chomwecho pamaso pa akulu a Israele. 7Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?
Aisraele apambana Amaleke
8Pamenepo anadza Amaleke, nayambana ndi Israele m'Refidimu. 9Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleke; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa. 10Ndipo Yoswa anachita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleke; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa chitunda. 11#1Tim. 2.8Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lake Israele analakika; koma pamene anatsitsa dzanja lake Amaleke analakika. 12Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litalowa dzuwa. 13Ndipo Yoswa anathyola Amaleke ndi anthu ake ndi ku ukali kwa lupanga. 14#Num. 24.20; 1Sam. 15.3Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo. 15Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalitcha dzina lake Yehova Nisi: 16nati, Yehova walumbira: padzakhala nkhondo ya Yehova pa Amaleke m'mibadwomibadwo.
Currently Selected:
EKSODO 17: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi