EKSODO 16
16
Zinziri ndi mana
1Ndipo anachoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israele linalowa m'chipululu cha Sini, ndicho pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito. 2#Eks. 15.24; 1Ako. 10.10Ndipo khamu lonse la ana a Israele linadandaulira Mose ndi Aroni m'chipululu 3nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m'chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala. 4#Mas. 105.40; Yoh. 6.31-32Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'chilamulo changa kapena iai. 5Ndipo kudzakhala tsiku lachisanu ndi chimodzi, kuti azikonza umene adabwera nao, ataonjezapo muyeso unzake wa pa tsiku limodzi. 6Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israele, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakutulutsani m'dziko la Ejipito; 7#Yes. 40.5ndi m'mawa mwake mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife chiyani, kuti mutidandaulira ife? 8Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova. 9Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu. 10Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele kuti iwo anatembenukira kuchipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo. 11Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, 12Ndamva madandaulo a ana a Israele; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 13Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m'mawa padagwa mame pozungulira tsasa. 14Ndipo atasansuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa chipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati chipale panthaka. 15#Yoh. 6.31, 49, 58Ndipo pamene ana a Israele anakaona, anati wina ndi mnzake, Nchiyani ichi? Pakuti sanadziwe ngati nchiyani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale chakudya chanu. 16Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwake. 17Ndipo ana a Israele anatero, naola wina wambiri, wina pang'ono. 18#2Ako. 8.15Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalira, ndi iye amene adaola pang'ono sunamsowa; yense anaola monga mwa njala yake. 19Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m'mawa. 20Koma sanammvere Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao. 21Ndipo anauola m'mawa ndi m'mawa, yense monga mwa njala yake; popeza likatentha dzuwa umasungunuka. 22Ndipo kunali tsiku lachisanu ndi chimodzi, anaola mkate, naonjezapo linzake, maomeri awiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose. 23#Gen. 2.3Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziocha, ochani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa. 24Ndipo anausunga kufikira m'mawa, monga adalamulira Mose; koma sunanunkha, ndipo sunagwa mphutsi. 25Ndipo Mose anati, Muudye lero; pakuti lero ndilo Sabata la Yehova; simuupeza lero pabwalo. 26Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe. 27Ndipo kunali tsiku la Sabata, kuti anthu ena anatuluka kukaola, koma sanaupeze. 28#2Maf. 17.14Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira liti? 29Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m'malo mwake munthu asatuluke m'malo mwake tsiku lachisanu ndi chiwiri. 30Ndipo anthu anapumula tsiku lachisanu ndi chiwiri. 31Ndipo mbumba ya Israele inautcha dzina lake Mana; ndiwo ngati zipatso zampasa, oyera; powalawa akunga timitanda tosanganiza ndi uchi. 32Ndipo Mose anati, Awa ndi mau anauza Yehova, Dzazani omeri nao, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nao m'chipululu, muja ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito. 33#Aheb. 9.4Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mphika, nuthiremo mana odzala omeri, nuuike pamaso pa Yehova, usungikire mibadwo yanu. 34Monga Yehova anauza Mose, momwemo Aroni anauika patsogolo pa Mboni, usungikeko. 35#Yos. 5.12Ndipo ana a Israele anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani. 36Koma omeri ndilo limodzi la magawo khumi la efa.
Currently Selected:
EKSODO 16: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi