EKSODO 15
15
Nyimbo yolemekeza Mulungu
1 #
Ower. 5.1
Pamenepo Mose ndi ana a Israele anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti,
Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu;
kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.
2 #
Mas. 18.2; 118.28; 140.7 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga,
ndipo wakhala chipulumutso changa;
ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza;
ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.
3 #
Mas. 24.8
Yehova ndiye wankhondo;
dzina lake ndiye Yehova.
4Magaleta a Farao ndi nkhondo yake anawaponya m'nyanja;
ndi akazembe ake osankhika anamira m'Nyanja Yofiira.
5Nyanja inawamiza;
anamira mozama ngati mwala.
6 #
Mas. 118.15-16
Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu,
dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.
7Ndipo ndi ukulu wanu waukulu mwapasula akuukira Inu;
mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati chiputu.
8 #
Yob. 4.9
Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika,
mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu;
zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.
9Mdani anati,
Ndiwalondola, ndiwapeza,
ndidzagawa zofunkha;
ndidzakhuta nao mtima;
ndidzasolola lupanga langa,
dzanja langa lidzawaononga.
10Munaombetsa mphepo yanu, nyanja inawamiza;
anamira m'madzi aakulu ngati mtovu.
11 #
2Sam. 7.22; Yes. 6.3 Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova?
Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera,
woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?
12Mwatambasula dzanja lanu lamanja,
nthaka inawameza.
13 #
Mas. 77.20
Mwa chifundo chanu mwatsogolera anthu amene mudawaombola;
mwamphamvu yanu mudawalondolera
njira yakunka pokhala panu poyera.
14Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira;
kuda mtima kwagwira anthu okhala m'Filistiya.
15Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa;
agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Mowabu;
okhala m'Kanani onse asungunuka mtima.
16 #
Yos. 2.9; Yes. 43.1, 3 Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera;
pa dzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala;
kufikira apita anthu anu, Yehova,
kufikira apita anthu amene mudawaombola.
17Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka pa phiri la cholowa chanu,
pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova,
malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika.
18 #
Mas. 10.16
Yehova adzachita ufumu nthawi yonka muyaya.
19Pakuti akavalo a Farao analowa m'nyanja, ndi magaleta ake ndi apakavalo ake, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m'nyanja; koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja. 20#Ower. 4.4; 1Sam. 18.6Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.
21Ndipo Miriyamu anawayankha,
Imbirani Yehova, pakuti wapambanatu;
kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.
Madzi a ku Mara
22Ndipo Mose anatsogolera Israele kuchokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anatulukako nalowa m'chipululu cha Suri; nayenda m'chipululu masiku atatu, osapeza madzi. 23#Rut. 1.20Pamene anafika ku Mara sanakhoze kumwa madzi a Mara, pakuti anali owawa; chifukwa chake anatcha dzina lake Mara. 24#Eks. 16.2; 17.3Ndipo anthu anadandaulira Mose, ndi kuti, Tidzamwa chiyani? 25Ndipo iye anafuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m'madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi chiweruzo, ndi pomwepa anawayesa; 26#Mas. 103.3ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zoona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aejipito sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe.
27Ndipo anafika pa Elimu, ndi pamenepo panali akasupe a madzi khumi ndi awiri, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamanga chigono chao pomwepo pa madziwo.
Currently Selected:
EKSODO 15: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi