EKSODO 14
14
Farao alondola Aisraele
1Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti, 2Lankhula ndi anthu a Israele, kuti abwerere m'mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja. 3Ndipo Farao adzanena za ana a Israele, Azimidwa dziko, chipululu chawatsekera. 4#Eks. 14.17-18Ndipo ndidzalimbitsa mtima wake wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yake yonse; pamenepo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndipo anachita chomwecho. 5Ndipo anauza mfumu ya Aejipito kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ake inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ichi nchiyani tachita, kuti talola Israele amuke osatigwiriranso ntchito? 6Ndipo anamanga galeta lake, napita nao anthu ake; 7napita nao magaleta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magaleta onse a m'Ejipito, ndi akapitao ao onse. 8Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka. 9Ndipo Aejipito anawalondola, ndiwo akavalo ndi magaleta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni. 10#Mas. 34.17Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova. 11Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwatichotsera kuti tikafe m'chipululu chifukwa panalibe manda m'Ejipito? Nchiyani ichi mwatichitira kuti mwatitulutsa m'Ejipito? 12#Eks. 5.21Si awa mauwo tinalankhula nanu m'Ejipito ndi kuti, Tilekeni, kuti tigwirire ntchito Aejipito? Pakuti kutumikira Aejipito kutikomera si kufa m'chipululu ai. 13#Gen. 49.18; 2Mbi. 20.15; Yes. 41.10Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, chilimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aejipito mwawaona lerowa, simudzawaonanso konse. 14#Yos. 10.14; Yes. 30.15Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete.
Aisraele aoloka pouma
15Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa Ine? Lankhula ndi ana a Israele kuti aziyenda. 16Ndipo iwe nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigawe, kuti ana a Israele alowe pakati pa nyanja pouma. 17#Eks. 14.4Ndipo Ine, taonani, ndidzalimbitsa mitima ya Aejipito, kuti alowemo powatsata; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao, ndi pa nkhondo yake yonse, pa magaleta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake. 18Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, polemekezedwa Ine pa Farao, pa magaleta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake. 19#Yes. 63.9Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israele, unachokako, nutsata pambuyo pao; ndipo mtambo njo uja unachoka patsogolo pao, nuima pambuyo pao; 20nulowa pakati pa ulendo wa Aejipito ndi ulendo wa Aisraele; ndipo mtambo unachita mdima, komanso unaunikira usiku; ndipo ulendo wina sunayandikizana ndi unzake usiku wonse. 21Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum'mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana. 22#1Ako. 10.1; Aheb. 11.29Ndipo ana a Israele analowa pakati pa nyanja pouma; ndi madziwo anakhala kwa iwo ngati khoma palamanja, ndi palamanzere. 23Ndipo Aejipito anawalondola, nalowa pakati pa nyanja powatsata, ndiwo akavalo onse a Farao, magaleta ake, ndi apakavalo ake. 24Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m'moto ndi m'mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aejipito, nauvuta ulendo wa Aejipito. 25Ndipo anagulula njinga za magaleta ao, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aejipito anati, Tithawe pamaso pa Israele; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aejipito.
Aejipito amizidwa m'nyanja
26Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kunyanja, kuti madziwo abwerere kudzamiza Aejipito, magaleta ao, ndi apakavalo ao. 27Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja, ndi nyanja inabwerera m'mayendedwe ake mbandakucha; ndipo Aejipito pothawa anakomana nayo; ndipo Yehova anakutumula Aejipito m'kati mwa nyanja. 28#Mas. 78.53Popeza madziwo anabwerera, namiza magaleta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m'nyanja; sanatsale wa iwowa ndi mmodzi yense. 29Koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi lamanzere. 30Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lomwelo m'manja a Aejipito; ndipo Israele anaona Aejipito akufa m'mphepete mwa nyanja. 31#Yoh. 2.11Ndipo Israele anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aejipito, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.
Currently Selected:
EKSODO 14: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi