DANIELE 9
9
Pemphero la Daniele
1 #
Dan. 1.21; 5.31; 6.28 Chaka choyamba cha Dariusi mwana wa Ahasuwero, wa mbeu ya Amedi, amene anamlonga mfumu ya Ababiloni; 2#2Mbi. 36.21; Yer. 25.11chaka choyamba cha ufumu wake, ine Daniele ndinazindikira mwa mabuku kuti chiwerengo chake cha zaka, chimene mau a Yehova anadzera nacho kwa Yeremiya mneneri, kunena za makwaniridwe a mapasuko a Yerusalemu, ndizo zaka makumi asanu ndi awiri. 3#Neh. 1.4-5Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m'pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa. 4Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi chifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu, 5#1Maf. 8.47, 48; Neh. 1.6tachimwa, tachita mphulupulu, tachita zoipa, tapanduka, kupatuka ndi kusiya maneno anu ndi maweruzo anu; 6sitinamvera atumiki anu aneneri, amene ananena m'dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m'dziko. 7#Neh. 9.33Ambuye, chilungamo ncha Inu, koma kwa ife manyazi a nkhope yathu, monga lero lino; kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, ndi kwa Aisraele onse okhala pafupi ndi okhala kutali, kumaiko onse kumene mudawaingira, chifukwa cha kulakwa kwao anakulakwirani nako. 8Ambuye, kwa ife kuli manyazi a nkhope yathu, kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, ndi kwa makolo athu; pakuti takuchimwirani. 9#Neh. 9.17; Mas. 130.4, 7Ambuye Mulungu wathu ndiye wachifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye; 10sitinamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malamulo ake anatiikirawo pamaso pathu, mwa atumiki ake aneneri. 11Inde Israele yense walakwira chilamulo chanu, ndi kupatuka, kuti asamvere mau anu; chifukwa chake temberero lathiridwa pa ife, ndi lumbiro lolembedwa m'chilamulo cha Mose mtumiki wa Mulungu; pakuti tamchimwira. 12Ndipo anakwaniritsa mau ake adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera choipa chachikulu; pakuti pansi pa thambo lonse sipanachitika monga umo panachitikira Yerusalemu. 13#Yes. 9.13Monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose choipa ichi chonse chatidzera; koma sitinapepeza Yehova Mulungu wathu, ndi kubwera kuleka mphulupulu zathu, ndi kuchita mwanzeru m'choonadi chanu. 14Chifukwa chake Yehova wakhala maso pa choipacho, ndi kutifikitsira icho; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu ntchito zake zonse azichita; ndipo sitinamvera mau ake. 15#Eks. 6.1, 6; Dan. 9.5Ndipo tsopano, Ambuye Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu m'dziko la Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino, tachimwa, tachita choipa. 16#Eks. 20.5; Mas. 31.1; 71.2; Dan. 9.20Ambuye, monga mwa chilungamo chanu chonse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zichoke kumudzi wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zochimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka chotonza cha onse otizungulira. 17#Mas. 67.1; Dan. 9.19Ndipo tsopano, Mulungu wathu, mumvere pemphero la mtumiki wanu, ndi mapembedzero ake, nimuwalitse nkhope yanu pa malo anu opatulika amene ali opasuka, chifukwa cha Ambuye. 18#Yes. 37.17; Yer. 25.29Mulungu wanga, tcherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mudzi udatchedwawo dzina lanu; pakuti dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, chifukwa cha ntchito zathu zolungama, koma chifukwa cha zifundo zanu zochuluka. 19#Mas. 79.9Ambuye, imvani; Ambuye khululukirani; Ambuye, mverani nimuchite; musachedwa, chifukwa cha inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mudzi wanu ndi anthu anu anatchedwa dzina lanu.
Masabata makumi asanu ndi awiriwo, ndi Wodzozedwayo
20Ndipo pakunena ine, ndi kupemphera, ndi kuvomereza tchimo langa, ndi tchimo la anthu a mtundu wanga Israele, ndi kutula chipembedzero changa pamaso pa Yehova Mulungu wanga, chifukwa cha phiri lopatulika la Mulungu wanga; 21#1Maf. 18.36; Dan. 8.16inde pakunena ine m'kupemphera, munthu uja Gabriele, amene ndidamuona m'masomphenya poyamba paja, anauluka mwaliwiro nandikhudza ngati nthawi yakupereka nsembe ya madzulo. 22Ndipo anandilangiza ine, ndi kulankhula nane, nati, Daniele iwe, ndatuluka tsopano ine kukuzindikiritsa mwaluntha. 23#Dan. 10.11, 19Pakuyamba iwe mapembedzero ako, linatuluka lamulo; ndipo ndadza ine kukufotokozera; pakuti ukondedwa kwambiri; zindikira tsono mau awa, nulingirire masomphenyawo. 24#Yes. 53.10; Aheb. 9.12Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu a mtundu wako ndi mudzi wako wopatulika, kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza, ndi kukhomera chizindikiro masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulika kwambiri. 25#Yoh. 1.41; 4.25Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto. 26#Yes. 53.8; Mat. 24.2; Mrk. 9.12; Luk. 19.44Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mudzi ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu. 27#Mat. 24.15; Mrk. 13.14; Luk. 21.20Ndipo iye adzapangana chipangano cholimba ndi ambiri sabata limodzi; ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa; ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira chimaliziro cholembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo.
Currently Selected:
DANIELE 9: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi