DANIELE 6
6
Akalonga amtchulira Daniele chifukwa kwa Dariusi
1Kudamkomera Dariusi kuikira ufumuwo akalonga zana limodzi mphambu makumi awiri akhale m'madera onse a ufumu; 2ndi akuyang'anira iwo akulu atatu, woyamba wao ndi Daniele; kuti akalonga awa adziwerengere kwa iwo, ndi kuti za mfumu zisasoweke. 3Pamenepo Daniele amene anaposa akuluwa ndi akalonga, popeza munali mzimu wopambana mwa iye, ndi mfumu inati imuike woyang'anira ufumu wonse. 4#Mlal. 4.4Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye. 5Pamenepo anthu awa anati, Sitidzamtola chifukwa chilichonse Daniele amene, tikapanda kumtola ichi pa chilamulo cha Mulungu wake. 6Ndipo akulu awa ndi akalonga anasonkhana kwa mfumu mofulumira, natero nayo, Mfumu Dariusi, mukhale ndi moyo chikhalire. 7Akulu onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lachifumu, ndi kuikapo choletsa cholimba, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango. 8#Est. 1.19Tsopano, mfumu, mukhazikitse choletsacho, ndi kutsimikiza cholembedwacho, kuti chisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi, amene sasinthika. 9Momwemo mfumu Dariusi anatsimikiza cholembedwa ndi choletsacho. 10#1Maf. 8.44-45; Yon. 2.4; Mas. 55.17; Mac. 10.9Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse. 11Pamenepo anasonkhana anthu awa, napeza Daniele alikupemphera ndi kupembedza pamaso pa Mulungu wake. 12#Dan. 6.8Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za choletsacho cha mfumu, Kodi simunatsimikiza choletsacho, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Choona chinthuchi, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika. 13#Dan. 3.12Pamenepo anayankha, nati pamaso pa mfumu, Daniele uja wa ana a ndende a Yuda sasamalira inu, mfumu, kapena choletsa munachitsimikizacho; koma apempha pemphero lake katatu tsiku limodzi. 14#Mrk. 6.26Ndipo mfumu m'mene atamva mau awa anaipidwa kwambiri, naika mtima wake pa Daniele kuti amlanditse, nayesetsa mpaka polowa dzuwa kumlanditsa. 15#Dan. 6.8Koma anthu awa anasonkhana kwa mfumu, nati kwa mfumu, Dziwani, mfumu, kuti lamulo la Amedi ndi Aperisi, ndilo kuti choletsa chilichonse ndi lemba lililonse idazikhazikira mfumu, zisasinthike.
Daniele aponyedwa m'dzanja la mikango
16Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Daniele, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Daniele, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa. 17#Mat. 27.66Ndipo anatenga mwala, nauika pakamwa pa dzenje, niukomera mfumu ndi chosindikizira chake, ndi chosindikizira cha akulu ake, kuti kasasinthike kanthu ka Daniele. 18Pamenepo mfumu inamuka kuchinyumba chake, nichezera kusala usikuwo, ngakhale zoimbitsa sanabwere nazo pamaso pake, ndi m'maso mwake munamuumira. 19Nilawira mamawa mfumu, nimuka mofulumira kudzenje la mikango. 20#Dan. 3.15Ndipo poyandikira padzenje inafuula ndi mau achisoni mfumu, ninena, niti kwa Daniele, Daniele, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene umtumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwa mikango? 21Pamenepo Daniele anati kwa mfumu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire. 22#Dan. 3.28; Aheb. 11.33Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwa. 23#Aheb. 11.33Pamenepo mfumu inakondwera kwambiri, niwauza atulutse Daniele m'dzenje. Momwemo anamtulutsa Daniele m'dzenje, ndi pathupi pake sipadaoneka bala, popeza anakhulupirira Mulungu wake. 24#Est. 9.10Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.
25 #
Dan. 4.1
Pamenepo mfumu Dariusi analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala pa dziko lonse lapansi, Mtendere uchulukire inu. 26#Mas. 99.1; Dan. 4.34; Luk. 1.33Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Daniele; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro. 27Iye apulumutsa, nalanditsa, nachita zizindikiro ndi zozizwa m'mwamba ndi pa dziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Daniele kumphamvu ya mikango. 28#Ezr. 1.1-2Momwemo Daniele amene anakuzikabe pokhala Dariusi mfumu, ndi pokhala mfumu Kirusi wa ku Persiya.
Currently Selected:
DANIELE 6: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi