DANIELE 3
3
Nebukadinezara apanga fano lagolide
1Mfumu Nebukadinezara anapanga fano lagolide, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi thunthu lake mikono isanu ndi umodzi; analiimika pa chidikha cha Dura, m'dera la ku Babiloni. 2Ndipo mfumu Nebukadinezara inatumiza kukasonkhanitsa akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, abwera kuzulula fanoli adaliimika mfumu Nebukadinezara. 3Pamenepo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, anasonkhanira kupereka fano adaliimika mfumu Nebukadinezara, naimirira pamaso pa fano adaliimika Nebukadinezara. 4Ndipo wolalikira anafuulitsa, kuti, Akulamulirani inu anthu, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, 5kuti pakumva inu mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, mugwadire ndi kulambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara; 6#Yer. 29.22ndipo aliyense wosagwadira ndi kulambira, adzaponyedwa nthawi yomweyo m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto. 7Potero nthawi yomweyo pakumva anthu onse mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi zoimbitsa zilizonse, anthu onse, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, anagwadira, nalambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara. 8Chifukwa chake anayandikira Ababiloni ena nthawi yomweyi, naneneza Ayuda. 9#Dan. 2.4Anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire. 10Inu mfumu mwalamulira kuti munthu aliyense amene adzamva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, agwadire, nalambire fanolo lagolide; 11ndi yense wosagwadira ndi kulambira adzaponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto. 12#Dan. 2.49Alipo Ayuda amene munawaika ayang'anire ntchito ya dera la ku Babiloni, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amuna awa, mfumu, sanasamalire inu, satumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo.
Anzake a Daniele aponyedwa m'ng'anjo yamoto
13Pamenepo Nebukadinezara, mumkwiyo ndi m'ukali wake, anawauza abwere nao Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. Ndipo anabwera nao amunawa kwa mfumu. 14Nebukadinezara anayankha, nati kwa iwo, Kodi mutero dala, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, kusatumikira milungu yanga, ndi kusalambira fano lagolide ndinaliimikalo? 15#Eks. 5.2; 2Maf. 18.35Mukavomereza tsono, pakumva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, chabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu amene adzakulanditsani m'manja mwanga ndani? 16#Mat. 10.19Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Sikufunika kuti tikuyankheni pa mlandu uwu. 17#Mac. 27.25Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu. 18#Mac. 5.29Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo. 19Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yake anansandulikira Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera. 20Nauza amuna ena amphamvu a m'khamu lake la nkhondo amange Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, ndi kuwaponya m'ng'anjo yotentha yamoto. 21Pamenepo amuna awa anamangidwa ali chivalire zofunda zao, malaya ao, ndi nduwira zao, ndi zovala zao zina; naponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto. 22Motero, popeza mau a mfumu anafulumiza, ndi ng'anjo inatentha koposa, lawi la moto linapha iwo aja ananyamula Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. 23Ndipo amuna atatu awa, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, anagwa pansi omangidwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto. 24Pamenepo mfumu Nebukadinezara anadabwa, nauka msanga, nanena nati kwa mandoda ake, Kodi sitinaponya amuna atatu omangidwa m'kati mwa moto? Anayankha nati kwa mfumu, Inde mfumu. 25#Mas. 34.7; Yes. 43.2; Dan. 3.28Anayankha, nati, Taonani, ndilikuona amuna anai omasuka, alikuyenda m'kati mwa moto; ndipo alibe kuphwetekwa, ndi maonekedwe a wachinai akunga mwana wa milungu. 26Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo la ng'anjo yotentha yamoto, analankhula, nati, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, inu atumiki a Mulungu Wam'mwambamwamba, tulukani, idzani kuno. Pamenepo Sadrake, Mesake, ndi Abedenego, anatuluka m'kati mwa moto. 27#Aheb. 11.34Ndipo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, ndi mandoda a mfumu, atasonkhana, anaona amuna awa, kuti moto unalibe mphamvu pa matupi ao, losawauka tsitsi la pamutu pao, ndi zofunda zao zosasandulika, fungo lomwe lamoto losawaomba. 28#Dan. 3.25; Yer. 17.7Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu waowao. 29#Dan. 6.27Chifukwa chake ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uliwonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, adzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero. 30Pamenepo mfumu inakuza Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, m'dera la ku Babiloni.
Currently Selected:
DANIELE 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi