YouVersion Logo
Search Icon

DANIELE 1

1
Maleredwe a Daniele ndi anzake kwa mfumu ya ku Babiloni
1 # 2Maf. 24.1 Chaka chachitatu cha Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adadza ku Yerusalemu, naumangira misasa ya nkhondo. 2#Gen. 10.10; 2Mbi. 36.7; Yer. 27.19-20Ndipo Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake. 3#2Maf. 20.17-18Ndipo mfumu inauza Asipenazi mkulu wa adindo kuti abwere nao ena a ana a Israele, a mbeu ya mafumu, ndi ya akalonga; 4anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni. 5Ndipo mfumu inawaikira gawo la chakudya cha mfumu tsiku ndi tsiku, ndi la vinyo wakumwa iye, ndi kuti awalere zaka zitatu, kuti potsiriza pake aimirire pamaso pa mfumu. 6Mwa awa tsono munali a ana a Yuda, Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya. 7Ndi mkulu wa adindo anawapatsa maina ena; Daniele anamutcha Belitesazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaele, Mesaki; ndi Azariya, Abedenego. 8#Ezk. 4.13; 1Ako. 9.27Koma Daniele anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya cha mfumu, kapena ndi vinyo amamwa; chifukwa chake anapempha mkulu wa adindo amlole asadzidetse. 9Ndipo Mulungu anamkometsera Daniele mtima wa mkulu wa adindo, amchitire chifundo. 10#Mas. 106.46Nati mkulu wa adindo kwa Daniele, Ine ndiopa mbuyanga mfumu, amene anakuikirani chakudya chanu ndi chakumwa chanu; pakuti aonerenji nkhope zanu zachisoni zoposa za anyamata olingana ndi inu? Momwemo mudzapalamulitsa mutu wanga kwa mfumu. 11Nati Daniele kwa kapitao, amene mkulu wa adindo adamuikayo ayang'anire Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya, 12Muyesetu anyamata anu masiku khumi; atipatse zomera m'nthaka tidye, ndi madzi timwe. 13Pamenepo mupenye maonekedwe athu ndi maonekedwe a anyamata akudya chakudya cha mfumu; ndi monga umo muonera, muchitire anyamata anu. 14Ndipo anawamvera mau awa, nawayesa masiku khumi. 15Atatha masiku khumiwo tsono, anaona kuti maonekedwe ao ndi kunenepa kwao anaposa anyamata onse adadyawo zakudya za mfumu. 16Pamenepo kapitaoyo anachotsa chakudya chao ndi vinyo akadamwa, nawapatsa zomera m'nthaka. 17#1Maf. 3.12; Yak. 1.5Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse. 18Atatha masiku inanenawo mfumu kuti alowe nao, mkulu wa adindo analowa nao pamaso pa Nebukadinezara. 19Ndipo mfumu inalankhula nao, koma mwa iwo onse sanapezeke monga Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya; naimirira iwo pamaso pa mfumu. 20Ndipo m'mau ali onse anzeru ndi aluntha, amene mfumu inawafunsira. Inawapeza akuposa alembi ndi openda onse m'ufumu wake wonse. 21Nakhala moyo Daniele mpaka chaka choyamba cha mfumu Kirusi.

Currently Selected:

DANIELE 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in