MACHITIDWE A ATUMWI 18
18
Paulo ku Korinto ndi ku Efeso. Abwera ku Yerusalemu
1Zitapita izi anachoka ku Atene, nadza ku Korinto. 2Ndipo anapeza Myuda wina dzina lake Akwila, fuko lake la ku Ponto, atachoka chatsopano ku Italiya, pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudio analamulira Ayuda onse achoke m'Roma; ndipo Paulo anadza kwa iwo: 3#Mac. 20.34ndipo popeza anali wa ntchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira ntchito; pakuti ntchito yao inali yakusoka mahema. 4#Mac. 17.2Ndipo anafotokozera m'sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Agriki.
5 #
Mac. 18.28
Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu. 6#Mac. 13.46Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu. 7Ndipo anachoka kumeneko, nalowa m'nyumba ya munthu, dzina lake Tito Yusto, amene anapembedza Mulungu, nyumba yake inayandikizana ndi sunagoge. 8Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupirira, nabatizidwa. 9#Mac. 23.11Ndipo Ambuye anati kwa Paulo usiku m'masomphenya, Usaope, koma nena, usakhale chete; 10#Mat. 28.20chifukwa Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuipse; chifukwa ndili nao anthu ambiri m'mudzi muno. 11Ndipo anakhala komwe chaka chimodzi kudza miyezi isanu ndi umodzi; naphunzitsa mau a Mulungu mwa iwo.
12Tsono pamene Galio anali chiwanga cha Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye kumpando wachiweruziro, 13kuti, Uyu akopa anthu apembedze Mulungu pokana chilamulo. 14#Mac. 23.29Koma pamene Paulo anati atsegule pakamwa pake, Galio anati kwa Ayuda, Ukadakhala mlandu wa chosalungama, kapena dumbo loipa, Ayuda inu, mwenzi nditakumverani inu; 15koma akakhala mafunso a mau ndi maina ndi chilamulo chanu; muyang'ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi. 16Ndipo anawapirikitsa pa mpando wachiweruziro. 17#Mac. 18.12Ndipo anamgwira Sostene, mkulu wa sunagoge, nampanda kumpando wachiweruziro. Ndipo Galio sanasamalira zimenezi.
18 #
Num. 6.18, 21; Mac. 21.24 Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m'ngalawa ku Siriya, pamodzi naye Prisila ndi Akwila; popeza anameta mutu wake m'Kenkrea; pakuti adawinda. 19Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda. 20Pamene iwo anamfunsa iye kuti akhale nthawi ina yoenjezerapo, sanavomereza; 21koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa. 22Ndipo pamene anakocheza pa Kesareya, anakwera naulonjera Mpingo, natsikira ku Antiokeya. 23Atakhala kumeneko nthawi, anachoka, napita ku madera osiyanasiyana a dziko la Galatiya ndi la Frijiya, nakhazikitsa ophunzira onse.
Apolo ku Efeso ndi Korinto
24Ndipo anafika ku Efeso Myuda wina dzina lake Apolo, fuko lake la ku Aleksandriya, munthu wolankhula mwanzeru; ndipo anali wamphamvu m'malembo. 25#Mac. 19.3Iyeyo anaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha; 26#Mac. 18.2ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Prisila ndi Akwila, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa. 27#1Ako. 3.6Ndipo pamene iye anafuna kuoloka kunka ku Akaya, abale anamfulumiza, ndi kulembera akalata kwa ophunzira kuti amlandire: ndipo pamene anafika, iye anathangata ndithu iwo akukhulupirira mwa chisomo; 28#Mac. 23.29pakuti ndi mphamvu anatsutsa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Khristu.
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 18: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi