YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 16

16
1 # 1Tim. 1.1-2; 2Tim. 1.5 Ndipo anafikanso ku Deribe ndi Listara; ndipo taonani, panali wophunzira wina pamenepo, dzina lake Timoteo, amake ndiye Myuda wokhulupirira; koma atate wake ndiye Mgriki. 2Ameneyo anamchitira umboni wabwino abale a ku Listara ndi Ikonio. 3#1Ako. 9.20Iyeyo Paulo anafuna kuti amuke naye, ndipo anamtenga, namdula, chifukwa cha Ayuda amene anakhala m'maikomo; pakuti onse anadziwa kuti atate wake anali Mgriki. 4#Mac. 15.28-29Pamene anapita kupyola pamidzi, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamulira atumwi ndi akulu a pa Yerusalemu. 5#Mac. 15.41Kotero Mipingoyo inalimbikitsidwa m'chikhulupiriro, nachuluka m'chiwerengo chao tsiku ndi tsiku.
6Ndipo anapita pa dziko la Frijiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau m'Asiya; 7pamene anafika kundunji kwa Misiya, anayesa kunka ku Bitiniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza; 8#2Ako. 2.12-13ndipo pamene anapita pambali pa Misiya, anatsikira ku Troasi.
Masomphenya a ku Troasi. Paulo aoloka nalalikira ku Filipi. Za Lidia wogulitsa chibakuwa. Mdindo wa ku Filipi
9 # 2Ako. 2.12-13 Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Masedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Masedoniya kuno, mudzatithangate ife. 10#2Ako. 2.12-13Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kutulukira kunka ku Masedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.
11Chotero tinachokera ku Troasi m'ngalawa, m'mene tinalunjikitsa ku Samotrase, ndipo m'mawa mwake ku Neapoli; 12pochokera kumeneko tinafika ku Filipi, mudzi wa ku Masedoniya, waukulu wa m'dzikomo, wa milaga ya Roma; ndipo tidagona momwemo masiku ena. 13Tsiku la Sabata tinatuluka kumudzi kunka kumbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana. 14Ndipo anatimva mkazi wina dzina lake Lidia, wakugulitsa chibakuwa, wa kumudzi wa Tiatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wake Ambuye anatsegula; kuti amvere zimene anazinena Paulo. 15#Gen. 19.3; Luk. 24.29Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.
16 # 1Sam. 28.7 Ndipo panali, pamene tinali kunka kukapemphera, anakomana ndi ife mdzakazi wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake. 17Ameneyo anatsata Paulo ndi ife, nafuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso. 18#Mrk. 1.25, 34; 16.17Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo.
19 # Mat. 10.18; Mac. 19.25-26; 2Ako. 2.12-13 Koma pamene ambuye ake anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Silasi, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akulu, 20ndipo pamene adanka nao kwa oweruza, anati, Anthu awa avuta kwambiri mudzi wathu, ndiwo Ayuda, 21ndipo alalikira miyambo imene siiloleka ife kuilandira, kapena kuichita, ndife Aroma. 22#2Ako. 6.5Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang'ambira malaya ao; nalamulira kuti awakwapule. 23Pamene anawaonetsa mikwingwirima yambiri, anawaika m'ndende, nauza mdindo kuti awasunge bwino. 24Pakumva iye kulamulira kotero anawaika m'chipinda cha m'kati, namangitsa mapazi ao m'zigologolo. 25Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva; 26#Mac. 4.31; 5.19; 12.7, 10ndipo mwadzidzidzi panali chivomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka. 27Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am'ndende adathawa. 28Koma Paulo anafuula ndi mau akulu, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tili muno. 29Ndipo mdindo anaitanitsa nyali, natumphira m'kati, alinkunthunthumira ndi mantha, nagwa pamaso pa Paulo ndi Silasi, 30#Mac. 2.37nawatulutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke? 31#Yoh. 3.16, 36; 1Yoh. 5.10Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako. 32Ndipo anamuuza iye mau a Ambuye, pamodzi ndi onse a pabanja pake. 33Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake. 34Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwake, nawakhazikira chakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pake, atakhulupirira Mulungu.
35Kutacha, oweruza anatumiza akapitao, kuti, Mukamasule anthu aja. 36Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu tulukani, mukani mumtendere. 37#Mac. 22.25Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ife pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ife amene tili Aroma, natiika m'ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira ife m'tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atitulutse. 38Ndipo akapitao anafotokozera mauwo kwa oweruza; ndipo iwowo anaopa, pakumva kuti anali Aroma. 39#Mat. 8.34Ndipo anadza nawapembedza; ndipo pamene anawatulutsa, anawapempha kuti achoke pamudzi. 40#Mac. 16.14Ndipo anatuluka m'ndendemo, nalowa m'nyumba ya Lidia: ndipo pamene anaona abale, anawasangalatsa, namuka.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in