1
MACHITIDWE A ATUMWI 16:31
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.
Compare
Explore MACHITIDWE A ATUMWI 16:31
2
MACHITIDWE A ATUMWI 16:25-26
Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva; ndipo mwadzidzidzi panali chivomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka.
Explore MACHITIDWE A ATUMWI 16:25-26
3
MACHITIDWE A ATUMWI 16:30
nawatulutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke?
Explore MACHITIDWE A ATUMWI 16:30
4
MACHITIDWE A ATUMWI 16:27-28
Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am'ndende adathawa. Koma Paulo anafuula ndi mau akulu, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tili muno.
Explore MACHITIDWE A ATUMWI 16:27-28
Home
Bible
Plans
Videos