2 SAMUELE 24
24
Kuwerengedwa kwa anthu kuwatengera chilango cha Mulungu
1 #
1Mbi. 21.1-28; Yak. 1.13-14 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda. 2#Yer. 17.5Ndipo mfumu inanena ndi Yowabu kazembe wa khamu, amene anali naye, Kayendere tsopano mafuko onse a Israele, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, nuwerenge anthuwo, kuti ndidziwe kuchuluka kwao kwa anthu. 3Ndipo Yowabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwachulukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu achione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi chinthu ichi? 4Koma mau a mfumu anapambana Yowabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yowabu ndi atsogoleri a khamulo anatuluka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israele. 5Naoloka Yordani, namanga zithando ku Aroere ku dzanja lamanja kwa mudzi uli pakati pa chigwa cha Gadi, ndi ku Yazere; 6nafika ku Giliyadi ndi ku dera la Tatimuhodisi; nafika ku Dani-Yaana ndi kuzungulira, kufikira ku Sidoni, 7nafika ku linga la Tiro ndi kumidzi yonse ya Ahivi ndi ya Akanani; natulukira kumwera kwa Yuda ku Beereseba. 8Chomwecho pamene atayenda dziko lonse anafika ku Yerusalemu pakutha miyezi isanu ndi inai, ndi masiku makumi awiri. 9Ndipo Yowabu anapereka kwa mfumu kuchuluka kwa anthu adawawerenga; ndipo m'Israele munali anthu zikwi mazana asanu ndi atatu, ngwazi zosolola lupanga; ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi mazana asanu.
10 #
1Sam. 24.5; 2Sam. 12.13 Pamenepo mtima wa Davide unamtsutsa, atatha kuwerenga anthuwo. Davide nati kwa Yehova, Ndinachimwa kwakukulu ndi chinthu chimene ndinachita; koma tsopano Yehova muchotse mphulupulu ya mnyamata wanu, pakuti ndinachita kopusa ndithu. 11Ndipo pouka Davide m'mawa mau a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlauli wa Davide, kuti, 12Kalankhule ndi Davide, Atero Yehova, kuti, Ndikuikira zinthu zitatu; udzisankhire wekha chimodzi cha izo, ndikakuchitire chimenecho. 13Chomwecho Gadi anafika kwa Davide, namuuza nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupirikitsani miyezi itatu? Kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Chenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo. 14#Mas. 103.8, 13-14Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zake nzazikulu; koma tisagwe m'dzanja la munthu. 15Chomwecho Yehova anatumiza mliri pa Israele kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikira; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba. 16#Gen. 6.6; 1Sam. 15.11; Yow. 2.13-14Ndipo pamene mthenga anatambasulira dzanja lake ku Yerusalemu kuuononga, choipacho chinachititsa Yehova chisoni, Iye nauza mthenga wakuononga anthuwo, kuti, Kwafikira tsopano, bweza dzanja lako. Ndipo mthenga wa Yehova anali pa dwale la Arauna Myebusi. 17Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndachimwa ine, ndinachita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.
Davide ammangira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna
18Ndipo Gadi anafika tsiku lomwelo kwa Davide nanena naye, Kwerani mukamangire Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna Myebusi. 19Ndipo Davide anakwerako monga mwa kunena kwa Gadi, monga adalamulira Yehova. 20Ndipo Arauna anayang'ana naona mfumuyo ndi anyamata ake alikubwera kwa iye; natuluka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yake pansi. 21#Gen. 23.8-16; Num. 16.48, 50Arauna nati, Mbuye wanga mfumu, mwadzeranji kwa mnyamata wanu? Ndipo Davide, anati, Kugula dwale lako ili, kuti ndimangirepo Yehova guwa lansembe, kuti mliriwo ulekeke kwa anthu. 22Arauna nati kwa Davide Mbuye wanga mfumu atenge napereke nsembe chomkomera; siizi ng'ombe za nsembe yopsereza, ndi zipangizo ndi zomangira ng'ombe zikhale nkhuni; 23#Mas. 21.3; Ezk. 20.40-41zonsezi, mfumu, Arauna akupatsani mfumu. Ndipo Arauna anati kwa mfumu, Yehova Mulungu wanu akulandireni. 24Koma mfumu inati kwa Arauna, Iai; koma ndidzaligula kwa iwe pa mtengo wake, pakuti sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe zopsereza zopanda mtengo wake. Momwemo Davide anagula dwalelo ndi ng'ombezo naperekapo masekeli makumi asanu a siliva. 25#2Sam. 21.14Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka chifukwa cha dziko, ndi mliri wa pa Israele unalekeka.
Currently Selected:
2 SAMUELE 24: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi