1 MAFUMU Mau Oyamba
Mau Oyamba
Bukuli lotsatira 2 Samuele likupitiriza mbiri ya ufumu wa Israele kuyambira pa imfa ya Davide mpaka pa chaka ngati 850 BC.
Mau onena za mafumuwo aonetsa kuti mfumu ikakhala yokhulupirika kwa Mulungu, zake zimayenda bwino ndipo anthu ake amakhala pa mtendere; koma ikakhala yosamvera Mulungu ndi kumapembedza milungu ina, zinthu zimayenda moipa ndipo anthu amagwa m'mavuto ambiri. Mafumu akumpoto, ku Israele, analephera pa udindo wao; koma akum'mwera, ku Yuda, ena mwa iwo anali okanika, komabe ena anali okhulupirika. Pa masiku amenewo, Mulungu amatuma aneneri ake, anthu olimba mtima, kuti akachenjeze anthu ake, alekeretu kupembedza mafano ndipo azimvera Yehova Mulungu wao. Wina mwa iwo, wodziwika bwino anali Eliya amene anatsutsa ansembe otumikira Baala (mutu 18).
Za mkatimu
Davide atafa, mwana wake Solomoni alowa m'malo mwake 1.1—2.46
Ufumu wa Solomoni 3.1—11.43
a. Zaka zoyamba za ufumu wake 3.1—4.34
b. Amanga Kachisi wa Yehova 5.1—8.66
c. Zaka zotsiriza za ufumu wake 9.1—11.43
Ufumu wa Israele ugawika pawiri 12.1—22.53
a. Mafuko akumpoto aukira ufumu wa Rehobowamu 12.1—14.20
b. Mafumu olamulira Yuda ndi mafumu olamulira Israele 14.21—16.34
c. Mneneri Eliya 17.1—19.21
d. Mfumu Ahabu ya Israele 20.1—22.40
Mfumu Yehosafati ya Yuda ndi Mfumu Ahaziya ya Israele 22.41-53
Currently Selected:
1 MAFUMU Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi