YouVersion Logo
Search Icon

2 SAMUELE 12

12
Kulapa ndi kulangidwa kwa Davide
1 # Mas. 51 Ndipo Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Ndipo anafika kwa iye nanena naye, Pa mudzi wina panali anthu awiri; wina wolemera, wina wosauka. 2Wolemerayo anali nazo zoweta zazing'ono ndi zazikulu zambiri ndithu; 3koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kanadyako chakudya chake cha iye yekha, kanamwera m'chikho cha iye yekha, kanagona pa chifukato chake, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wake wamkazi. 4Ndipo kwa wolemerayo kunafika mlendo, ndipo iye analeka kutengako mwa zoweta zake zazing'ono ndi zazikulu, kuphikira mlendo amene anafika kwa iye, koma anatenga mwanawankhosa wa wosaukayo, naphikira munthu amene anafika kwa iye. 5Pamenepo mkwiyo wa Davide unayaka ndithu pa munthuyo, nati kwa Natani, Pali Yehova, munthu amene anachita ichi, ayenera kumupha; 6#Eks. 22.1; Luk. 19.8ndipo adzabwezera mwa mwanawankhosayo ena anai, chifukwa anachita ichi osakhala nacho chifundo.
7Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israele, ndinakupukumutsa m'dzanja la Saulo; 8ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako, ndi akazi a mbuye wako pa chifukato chako, ndinakupatsanso nyumba ya Israele ndi ya Yuda; ndipo zimenezi zikadakuchepera ndikadakuonjezera zina zakutizakuti. 9#2Sam. 11.15-17, 27Chifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kuchita chimene chili choipa pamaso pake? Unakantha Uriya Muhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wake akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni. 10Chifukwa chake tsono lupanga silidzachoka pa nyumba yako nthawi zonse, popeza unandipeputsa Ine, nudzitengera mkazi wa Uriya Muhiti akhale mkazi wako. 11#2Sam. 16.22Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzachotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa lili denene. 12Pakuti iwe unachichita m'tseri; koma Ine ndidzachita chinthu ichi pamaso pa Aisraele onse, dzuwa lili nde. 13#2Sam. 24.10; Mas. 32.1, 5; 51.4Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa. 14#Yes. 52.5; Ezk. 36.20, 23Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu. 15Ndipo Natani anamuka kwao. Ndipo Yehova anadwaza mwana amene mkazi wa Uriya anambalira Davide, nadwala kwambiri. 16#2Sam. 13.31Chifukwa chake Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi. 17Ndipo akulu a m'nyumba yake ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao. 18Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwanji kuti mwana wafa; sadzadzichitira choipa nanga? 19Koma pamene Davide anaona anyamata ake likunong'onezana, Davide anazindikira kuti mwanayo adafa; Davide nanena ndi anyamata ake, Kodi mwanayo wafa? Nati iwo, Wafa. 20#Yob. 1.20Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zovala; nafika kunyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika kunyumba yake; ndipo powauza anamuikira chakudya, nadya iye. 21Pamenepo anyamata ake ananena naye, Ichi mwachita nchiyani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya. 22Nati iye, Pamene mwanayo akali ndi moyo, ndinasala kudya ndi kulira, pakuti ndinati, Adziwa ndani kapena Yehova adzandichitira chifundo kuti mwanayo akhale ndi moyo. 23#Yob. 7.8-10Koma tsopano wafa, ndidzasaliranjinso kudya? Kodi ndikhoza kumbweza? Ine ndidzamuka kuli iye, koma iye sadzabweranso kwa ine.
Kubadwa kwa Solomoni
24 # 1Mbi. 22.9 Ndipo Davide anasangalatsa Bateseba mkazi wake, nalowa kwa iye, nagona naye; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Solomoni. Ndipo Yehova anamkonda iye, 25natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova.
26 # 1Mbi. 20.1-3 Ndipo Yowabu anathira nkhondo pa Raba wa ana a Amoni, nalanda mudzi wachifumu. 27Yowabu natumiza mithenga kwa Davide nati, Ndaponyana ndi Raba, inde ndalanda mudzi wa pamadzi. 28Chifukwa chake tsono musonkhanitse anthu otsalawo, nimumangire mudziwo zithando, muulande; kuti ine ndingalande mudziwo, ndipo ungatchedwe ndi dzina langa. 29Ndipo Davide anasonkhanitsa anthu onse, napita ku Raba, naponyana nao, naulanda. 30Nachotsa korona pa mutu wa mfumu yao; kulemera kwake kunali talente wa golide; ndipo m'menemo munali miyala ya mtengo wapatali; ndipo anamuika pa mutu wa Davide. Iye natulutsa zofunkha za mudziwo zambirimbiri. 31Natulutsa anthu a m'mudzimo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi nkhwangwa zachitsulo; nawapsitiriza ndi chitsulo, nawapititsa m'ng'anjo yanjerwa; natero ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwerera kunka ku Yerusalemu.

Currently Selected:

2 SAMUELE 12: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in