YouVersion Logo
Search Icon

2 SAMUELE 13

13
Tchimo loopsa la Aminoni
1 # 2Sam. 3.2-3 Ndipo kunali chitapita ichi, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wake wokongola, dzina lake ndiye Tamara, Aminoni mwana wa Davide anamkonda iye. 2Ndipo Aminoni anapsinjikadi nayamba kudwala chifukwa cha mlongo wake Tamara, pakuti anali namwali, ndipo Aminoni anachiyesa chapatali kumchitira kanthu. 3Koma Aminoni anali ndi bwenzi lake, dzina lake ndiye Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide. Ndipo Yonadabu anali munthu wochenjera ndithu. 4Nanena naye, Iwe mwana wa mfumu, uonderanji tsiku ndi tsiku? Sungandiuze kodi? Ndipo Aminoni anati kwa iye, Ndikonda Tamara, mlongo wa mbale wanga Abisalomu. 5Ndipo Yonadabu ananena naye, Ugone pa kama wako ndi kudzikokomera ulikudwala; ndipo pamene atate wako akadzakuona unene naye, Mulole mlongo wanga Tamara abwere kundipatsa kudya, nakonzere chakudyacho pamaso panga kuti ndichione ndi kuchidya cha m'manja mwake. 6Chomwecho Aminoni anagona, nadzikokomeza alikudwala; ndipo pamene mfumu inadza kumuona, Aminoni anati kwa mfumuyo, Mulole Tamara mlongo wanga abwere ndi kundipangira timitanda tiwiri pamaso panga, kuti ndikadye cha m'manja mwake. 7Ndipo Davide anatumiza mau kwao kwa Tamara, kuti, Upite kunyumba ya mlongo wako Aminoni, numkonzere chakudya. 8Chomwecho Tamara anapita kunyumba ya mlongo wake Aminoni; ndipo iye anali chigonere. Ndipo anatenga ufa naukanda naumba timitanda pamaso pake, nakazinga timitandato. 9#Gen. 45.1Ndipo anatenga chiwaya natitulutsa pamaso pake; koma anakana kudya. Ndipo Aminoni anati, Anthu onse atuluke kundisiya ine. Natuluka onse, kumsiya. 10Ndipo Aminoni anati kwa Tamara, Bwera nacho chakudya kuchipinda kuti ndikadye cha m'manja mwako. Ndipo Tamara anatenga timitanda anatipangato, nabwera nato kuchipinda kwa Aminoni mlongo wake. 11Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga. 12#Lev. 18.9, 11Koma iye anamyankha nati, Iai, mlongo wanga, usandichepetsa ine, pakuti chinthu chotere sichiyenera kuchitika m'Israele, usachita kupusa kumeneku. 13Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? Ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru m'Israele. Chifukwa chake tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine. 14Koma iye sadafuna kumvera mau ake, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkakamiza, nagona naye. 15Atatero Aminoni anadana naye ndi chidani chachikulu kopambana; pakuti chidani chimene anamuda nacho, chinali chachikulu koposa chikondi adamkonda nacho. Ndipo Aminoni ananena naye, Nyamuka, choka. 16Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti choipa ichi chakuti ulikundipirikitsa nchachikulu choposa china chija unandichitira ine. Koma anakana kumvera. 17Pomwepo anaitana mnyamata wake amene anamtumikira, nati, Tulutsa mkazi uyu kwa ine, nupiringidze chitseko atapita iye. 18Ndipo iye anavala chovala cha mawangamawanga, popeza ana akazi a mfumu okhala anamwali amavala zotere. Ndipo mnyamata wake anamtulutsa, napiringidza chitseko atapita iye. 19#Yos. 7.6; Yob. 2.12; Yer. 2.37Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pake, nang'amba chovala cha mawangamawanga chimene analikuvala, nagwira dzanja lake pamutu pake, namuka nayenda, nalira komveka. 20Ndipo Abisalomu mlongo wake ananena naye, Kodi mlongo wako Aminoni anali ndi iwe? Koma tsopano ukhale chete, mlongo wanga, iye ali mlongo wako; usavutika ndi chinthuchi. Chomwecho Tamara anakhala wounguluma m'nyumba ya Abisalomu mlongo wake. 21Koma pamene mfumu Davide anamva zonsezi, anakwiya ndithu. 22Ndipo Abisalomu sanalankhule ndi Aminoni chabwino kapena choipa, pakuti Abisalomu anamuda Aminoni popeza adachepetsa mlongo wake Tamara.
23Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali nao osenga nkhosa zake ku Baala-Hazori pafupi pa Efuremu; ndipo Abisalomu anaitana ana amuna onse a mfumu. 24Abisalomu nafika kwa mfumu nati, Onani, ine mnyamata wanu ndili nao osenga nkhosa; inu mfumu ndi anyamata anu mupite nane mnyamata wanu. 25Ndipo mfumu inati kwa Abisalomu, Iai mwana wanga, tisapite tonse, kuti tingakuchulukire. Ndipo iye anaiumirira koma inakana kupita; koma inamdalitsa. 26Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Aminoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, Iye apitirenji nawe? 27Koma Abisalomu anaiumirira iyo, nilola kuti Aminoni ndi ana amuna onse a mfumu apite naye. 28Ndipo Abisalomu anakamulira anyamata ake, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Aminoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Aminoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, chitani chamuna. 29Ndipo anyamata a Abisalomu anamchitira Aminoni monga umo Abisalomu anawalamulira. Pomwepo ana amuna onse a mfumu ananyamuka, nakwera munthu yense pa nyuru yake, nathawa. 30Ndipo kunali akali panjira, mau anafika kwa Davide, kuti, Abisalomu anapha ana amuna onse a mfumu, osatsalapo ndi mmodzi yense. 31#2Sam. 12.16Pamenepo mfumu inanyamuka ning'amba zovala zake nigona pansi, ndipo anyamata ake onse anaimirirapo ndi zovala zao zong'ambika. 32#2Sam. 13.3Ndipo Yonadabu mwana wa Simea mbale wa Davide anayankha nati, Mbuye wanga asaganize kuti anapha anyamata onse, ana amuna a mfumu, pakuti Aminoni yekha wafa, pakuti ichi chinatsimikizika ndi mau a Abisalomu kuyambira tsiku lija anachepetsa mlongo wake Tamara. 33Chifukwa chake tsono mfumu mbuye wanga asasauke mtima ndi chinthuchi, ndi kuganiza kuti ana amuna onse a mfumu afa; pakuti Aminoni yekha wafa. 34Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri. 35Ndipo Yonadabu ananena ndi mfumu, Onani, ana amuna a mfumu afika; monga ananena mnyamata wanu, momwemo. 36Ndipo kunali pakutsiriza iye kulankhula, onani, pomwepo ana amuna a mfumu anafika, nakweza mau ao, nalira misozi; ndi mfumu yomwe ndi anyamata ake analira ndi kulira kwakukulu ndithu. 37Koma Abisalomu anathawa, nanka kwa Talimai mwana wa Amihudi mfumu ya ku Gesuri. Ndipo Davide analira mwana wake tsiku ndi tsiku.
38Chomwecho anathawa Abisalomu, nanka ku Gesuri, nakakhala kumeneko zaka zitatu. 39Ndipo mfumu Davide analira kunka kwa Abisalomu, chifukwa anasangalatsidwa pa imfa ya Aminoni.

Currently Selected:

2 SAMUELE 13: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in