2 SAMUELE 1
1
Amuuza Davide za imfa ya Saulo
1 #
1Sam. 30.17, 26 Ndipo kunali atamwalira Saulo, pamene Davide anabwera atawapha Aamaleke, ndipo Davide atakhala ku Zikilagi masiku awiri; 2pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira. 3Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? Iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israele. 4Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? Undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Saulo ndi Yonatani mwana wake anafanso. 5Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwanji kuti Saulo ndi Yonatani mwana wake anafa? 6#1Sam. 31.1Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda pa phiri la Gilibowa, ndinaona, Saulo alikuyedzamira nthungo yake, ndi magaleta ndi apakavalo anamyandikiza. 7Ndipo iye pakucheukira m'mbuyo mwake anandiona, nandiitana. Ndipo ndinayankha, Ndine. 8Nanena, Ndiwe yani? Ndipo ndinayankha kuti, Ndine Mwamaleke. 9Ndipo anati kwa ine, Uime pa ine nundiphe, chifukwa kuwawa mtima kwandigwera ine, popeza ndikali moyobe. 10#Ower. 9.54M'mwemo ndinakhala pambali pake ndi kumtsiriza chifukwa ndinadziwa kuti sangakhalenso ndi moyo wake, atagwa. Ndipo ndinatenga korona wa pamutu pake, ndi chigwinjiri cha pa mkono wake, ndabwera nazo kuno kwa mbuye wanga. 11#2Sam. 3.31Pomwepo Davide anagwira zovala zake nazing'amba; nateronso anthu onse okhala naye. 12Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga. 13Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuzayo, Kwanu nkuti? Nayankha, Ine ndine mwana wa mlendo, Mwamaleke. 14#1Sam. 24.6; 26.9Ndipo Davide ananena naye, Bwanji sunaopa kusamula dzanja lako kuononga wodzozedwa wa Yehova? 15Davide naitana wina wa anyamatawo, nati, Sendera numkanthe. Ndipo anamkantha, nafa iye. 16#1Maf. 2.32, 37; Mat. 27.25Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; chifukwa pakamwa pako padachita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova.
Davide alirira Saulo ndi Yonatani
17Ndipo Davide analirira Saulo ndi Yonatani mwana wake ndi nyimbo iyi ya maliro; 18nawauza aphunzitse ana Ayuda nyimbo iyi ya Uta, onani inalembedwa m'buku la Yasara,
19Ulemerero wako, Israele, unaphedwa pa misanje yako.
Ha! Adagwa amphamvu!
20 #
1Sam. 31.9; Mik. 1.10 Usachinene ku Gati,
usachibukitse m'makwalala a Asikeloni,
kuti ana akazi a Afilisti angasekere,
kuti ana akazi a osadulidwawo angafuule mokondwera.
21Mapiri inu a Gilibowa,
pa inu pasakhale mame kapena mvula,
kapena minda yakutengako zopereka.
Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa,
chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.
22Uta wa Yonatani sunabwerera,
ndipo lupanga la Saulo silinabwerera chabe,
pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.
23Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao,
ndipo m'imfa yao sanasiyane;
anali nalo liwiro loposa chiombankhanga,
anali amphamvu koposa mikango.
24Ana akazi inu a Israele, mulirire Saulo,
amene anakuvekani ndi zofiira zokometsetsa,
amene anaika zokometsetsa zagolide pa zovala zanu.
25Ha! Amphamvuwo anagwa pakati pa nkhondo!
Yonatani anaphedwa pamisanje pako.
26 #
1Sam. 18.1, 3 Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe,
mbale wanga Yonatani;
wandikomera kwambiri;
chikondi chako, ndinadabwa nacho,
chinaposa chikondi cha anthu akazi.
27 #
2Sam. 1.19, 25 Ha! Amphamvuwo anagwa,
ndi zida za nkhondo zinaonengeka.
Currently Selected:
2 SAMUELE 1: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi