YouVersion Logo
Search Icon

2 MAFUMU 2

2
Eliya atengedwa kunka kumwamba
1 # Gen. 5.24 Ndipo kunali, pamene Yehova adati akweze Eliya kumwamba ndi kamvulumvulu, Eliya anachokera ku Giligala pamodzi ndi Elisa. 2Ndipo Eliya anati kwa Elisa, Ukhale pompano pakuti Yehova wandituma ndinke ku Betele. Nati Elisa, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Motero anatsikira iwo ku Betele. 3Ndipo ana a aneneri okhala ku Betele anatulukira Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati, Inde ndidziwa, khalani muli chete. 4Ndipo Eliya anati kwa iye, Elisa, ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yeriko. Nati iye, Pali Yehova, pali inu, sindikusiyani. Motero anadza ku Yeriko. 5Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli chete. 6Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordani. Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri. 7Ndipo anthu makumi asanu a ana a aneneri anapita, naima patali pandunji pao, iwo awiri naima ku Yordani. 8#Eks. 14.21; Yos. 3.16Ndipo Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma. 9Ndipo kunali ataoloka, Eliya anati kwa Elisa, Tapempha chimene ndikuchitire ndisanachotsedwe kwa iwe. Ndipo Elisa anati, Mundipatse magawo awiri a mzimu wanu akhale pa ine. 10Nati iye, Wapempha chinthu chapatali, koma ukandipenya pamene ndichotsedwa kwa iwe, kudzatero nawe; koma ukapanda kundipenyapo, sikudzatero ai. 11#2Maf. 6.17Ndipo kunachitika, akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka galeta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kamvulumvulu. 12#2Maf. 13.14Ndipo Elisa anapenya, nafuula, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zovala zakezake, nazing'amba pakati.
Elisa mneneri, zozizwitsa zake
13Pamenepo anatola chofunda chake cha Eliya chidamtayikiracho, nabwerera, naima m'mphepete mwa Yordani. 14#2Maf. 2.8Ndipo anatenga chofunda cha Eliya chidamtayikiracho, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa. 15Ndipo pamene anampenya ana a aneneri okhala ku Yeriko pandunji pake, anati, Mzimu wa Eliya watera pa Elisa. Ndipo anadza kukomana naye, nadziweramitsa pansi kumaso kwake. 16#1Maf. 18.12; Ezk. 8.3; Mac. 8.39Ndipo ananena naye, Taonani, tsono anyamata anufe tili nao amuna makumi asanu amphamvu, amuke kukafuna mbuye wanu; kapena wamkweza mzimu wa Yehova ndi kumponya pa phiri lina, kapena m'chigwa china. Koma anati, Musatumiza. 17Koma anamuumiriza kufikira anachita manyazi; pamenepo anati, Tumizani. Motero anatumiza amuna makumi asanu, namfunafuna iwo masiku atatu, osampeza. 18Nabwerera kwa iye ali chikhalire ku Yeriko, ndipo anati kwa iwo, Kodi sindinanena nanu, Musamuka?
19Ndipo amuna akumudzi anati kwa Elisa, Taonani, pamudzi pano mpabwino, monga umo aonera mbuye wanga; koma madzi ndi oipa, ndi nthaka siibalitsa. 20Pamenepo anati, Nditengereni chotengera chatsopano, muikemo mchere. Ndipo anabwera nacho kwa iye. 21#Eks. 15.25; 2Maf. 4.41; 6.6Ndipo anatuluka kunka ku magwero a madzi, nathiramo mchere, nati, Atero Yehova, Ndachiritsa madzi awa, sikudzafumirakonso imfa, kapena kusabalitsa. 22Chotero madzi anachiritsidwa mpaka lero lino, monga mwa mau a Elisa ananenawo.
23Ndipo anachokako kukwera ku Betele, ndipo iye ali chikwerere m'njiramo, munatuluka anyamata ang'ono m'mudzimo, namseka, nati kwa iye, Takwera wadazi, takwera wadazi! 24Ndipo anacheuka, nawaona, nawatemberera m'dzina la Yehova. Ndipo kuthengo kunatuluka zimbalangondo ziwiri zazikazi, ndi kupwetedza mwa iwo ana makumi anai mphambu awiri. 25Ndipo anachokako kunka kuphiri la Karimele; nabwera kumeneko nafika ku Samariya.

Currently Selected:

2 MAFUMU 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in