2 MAFUMU 1
1
Eliya ndi nthenda ya Ahaziya
1 #
2Sam. 8.2
Ndipo atamwalira Ahabu, Mowabu anapandukana ndi Israele. 2#1Sam. 5.10; 2Maf. 8.8Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pamwamba pa chipinda chake chosanja chinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni ngati ndidzachira nthenda iyi. 3Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti mukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? 4Chifukwa chake atero Yehova, Sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Nachoka Eliya. 5Ndipo mithenga inabwerera kwa iye, nanena nayo, Mwabwerera chifukwa ninji? 6Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. 7Ndipo iye ananena nayo, Nanga maonekedwe ake a munthu anakwerayo kukomana nanu, nanena nanu mau awa, ndi otani? 8#Zek. 13.4; Mat. 3.4Ninena naye, Ndiye munthu wovala zaubweya, namangira m'chuuno mwake ndi lamba lachikopa. Nati iye, Ndiye Eliya wa ku Tisibe. 9Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikali makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kunka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba pa phiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika. 10#Luk. 9.54Nayankha Eliya, nanena ndi mtsogoleriyo, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike moto wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo unatsika moto kumwamba, nunyeketsa iye ndi makumi asanu ake. 11Ndipo anabwereza kutuma kwa iye mtsogoleri wina ndi makumi asanu ake. Ndipo iye anayankha nanena naye, Munthu wa Mulungu iwe, itero mfumu, Tsika msanga. 12Nayankha Eliya, nanena nao, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike moto wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo moto wa Mulungu unatsika kumwamba nunyeketsa iye ndi makumi asanu ake. 13#1Sam. 26.21; Mas. 72.14Ndipo anabwerezanso kutuma mtsogoleri wachitatu ndi makumi asanu ake. Nakwera mtsogoleri wachitatuyo, nadzagwada ndi maondo ake pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wake pamaso panu. 14Taonani, watsika moto wakumwamba, nunyeketsa atsogoleri awiri oyamba aja pamodzi ndi makumi asanu ao; koma tsopano moyo wanga ukhale wa mtengo wake pamaso panu. 15Pamenepo mthenga wa Yehova anati kwa Eliya, Tsika naye, usamuopa. Nanyamuka iye, natsikira naye kwa mfumu. 16Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele kufunsira mau ake? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. 17Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m'malo mwake chaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna. 18Machitidwe ake ena tsono adawachita Ahaziya, sanalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?
Currently Selected:
2 MAFUMU 1: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi