2 MBIRI 33
33
Manase aikanso chipembedzo cha mafano
1 #
2Maf. 21.1-9
Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu zisanu. 2#Deut. 18.9; 2Mbi. 28.3Nachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawachotsa m'dziko mwao pamaso pa ana a Israele. 3#2Mbi. 30.14; 31.1Pakuti anamanganso misanje adaipasula Hezekiya atate wake, nautsira Abaala maguwa a nsembe, napanga zifanizo, nalambira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira. 4#1Maf. 8.29Namanga maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova, imene Yehova adati, M'Yerusalemu mudzakhala dzina langa kunthawi zonse. 5Namangiranso khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova. 6#2Mbi. 33.2Anapititsanso ana ake pamoto m'chigwa cha ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake. 7Ndipo anaika chifanizo chosema cha fanolo adachipanga m'nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomoni mwana wake, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha m'mafuko onse a Israele ndidzaika dzina langa kunthawi zonse; 8#2Sam. 7.10ndipo sindidzasunthanso phazi la Israele kudziko ndaliikira makolo anu; pokhapo asamalire kuchita zonse ndawalamulira, chilamulo chonse, ndi malemba, ndi maweruzo, mwa dzanja la Mose. 9Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu, kotero kuti anachita choipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israele.
Manase atengedwa kunka ku Babiloni, alapa nabwezedwa ku Yerusalemu
10Ndipo Yehova analankhula ndi Manase ndi anthu ake, koma sanasamalire. 11#2Maf. 20.16-17Motero Yehova anawafikitsira akazembe a khamu la nkhondo la mfumu ya Asiriya, namgwira Manase ndi zokowera, nammanga matangadza, namuka naye ku Babiloni. 12#1Pet. 5.6Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake. 13#Dan. 4.25Anampempha, ndipo anapembedzeka, namvera kupembedza kwake, nambwezera ku Yerusalemu m'ufumu wake. Pamenepo anadziwa Manase kuti Yehova ndiye Mulungu.
14Chitatha ichi tsono iye anaumangira mudzi wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'chigwa, mpaka polowera pa chipata chansomba; nazinga Ofele, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda. 15#2Mbi. 33.3, 5, 7Ndipo anachotsa milungu yachilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi m'Yerusalemu, nawataya kunja kwa mudzi. 16Namanga guwa la nsembe la Yehova, napherapo nsembe zamtendere ndi zoyamika, nalamulira Yuda atumikire Yehova Mulungu wa Israele. 17Koma anthu anapherabe nsembe pamisanje; koma anaziphera Yehova Mulungu wao. 18Machitidwe ena tsono a Manase, ndi pemphero lake kwa Mulungu wake, ndi mau a alauli akunena naye m'dzina la Yehova Mulungu wa Israele, taonani, zalembedwa m'machitidwe a mafumu a Israele. 19Pemphero lake lomwe, ndi m'mene Mulungu anapembedzeka naye, ndi tchimo lake lonse, ndi kulakwa kwake, ndi apo anamanga misanje, naimika zifanizo ndi mafano osema asanadzichepetse, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Hozai. 20Momwemo Manase anagona ndi makolo ake, namuika m'nyumba mwakemwake; ndi Amoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Amoni mfumu yoipayo
21 #
2Maf. 21.19-24
Amoni ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka ziwiri. 22Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira Manase atate wake; pakuti Amoni anaphera nsembe mafano osema onse amene adawapanga Manase atate wake, nawatumikira. 23Koma sanadzichepetse pamaso pa Yehova, monga umo anadzichepetsera Manase atate wake; koma Amoni amene anachulukitsa kupalamula kwake. 24Ndipo anyamata ake anampangira chiwembu, namupha m'nyumba yakeyake. 25Koma anthu a m'dziko anapha onse adampangira chiwembu mfumu Amoni; ndi anthu a m'dziko analonga Yosiya mwana wake akhale mfumu m'malo mwake.
Currently Selected:
2 MBIRI 33: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi