Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake. Anampempha, ndipo anapembedzeka, namvera kupembedza kwake, nambwezera ku Yerusalemu m'ufumu wake. Pamenepo anadziwa Manase kuti Yehova ndiye Mulungu.